Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUNGATANI KUTI MUCHEPETSE NKHAWA?

Mungatani Kuti Muchepetse Nkhawa?

Mungatani Kuti Muchepetse Nkhawa?

Kuti muchepetse nkhawa muyenera kuganizira zinthu zofunika kwambiri monga thanzi lanu, mmene mumachitira zinthu ndi ena komanso zolinga zomwe mumafuna mutazikwaniritsa. Munkhaniyi tikambirana njira zingapo zomwe zingakuthandizeni kuti muchepetse nkhawa.

Musamadere Nkhawa za Mawa

“Musamade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso.”​—MATEYU 6:34.

Mfundo yake: Kukhala ndi nkhawa ndi mbali ya moyo wathu. Komabe mukamaganizira zoti muchite lero, sibwino kumaderanso nkhawa kwambiri za mawa.

 • Kukhala ndi nkhawa kwambiri kungayambitse matenda a maganizo. Ndiye kodi mungatani? Choyamba, muyenera kudziwa kuti n’zosatheka kupeweratu nkhawa. Mukamangokhalira kudera nkhawa zinthu zomwe simungazipewe, mukhoza kupanikizika kwambiri. Chachiwiri, muyenera kudziwa kuti nthawi zambiri zinthu sizichitika mmene timaganizira.

Muzidziwa Zimene Mungakwanitse ndi Zomwe Simungakwanitse

“Nzeru yochokera kumwamba . . . ndi . . . yololera.”​—YAKOBO 3:17.

Mfundo yake: Musamayembekezere kuti inuyo kapena anthu ena azichita zinthu mosalakwitsa.

 • Muzizindikira zinthu zomwe inuyo kapena anthu ena sangakwanitse kuchita. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti musamapanikizike kwambiri komanso kuti zinthu zikuyendereni bwino. Komanso muzikonda kunena tinthabwala. Mukamasekaseka ngakhale pomwe zinthu zina zalakwika, simukhala ndi nkhawa.

Muzidziwa Zimene Zimakuchititsani Kukhala ndi Nkhawa

“Munthu wozindikira amakhala wofatsa.”​—MIYAMBO 17:27.

Mfundo yake: Kuganizira zinthu zodetsa nkhawa kungakuchitseni kuti musamaganize bwino. Choncho muziyesetsa kukhazika mtima pansi.

 • Muzidziwa zinthu zimene zimakupangitsani kukhala ndi nkhawa n’kuona zimene mumachita zikatero. Mwachitsanzo, mukakhala ndi nkhawa mungaone mmene mumaganizira, mmene mumamvera komanso zimene mumachita. Mukhoza kulemba zinthu zimenezi penapake. Izi zingakuthandizeni kudziwa zoyenera kuchita kuti musamakhale ndi nkhawa kwambiri. Ngati simungathe kuchita zimenezi, mungachite bwino kuganizira zimene mungachite kuti musamakhale ndi nkhawa kwambiri, mwina poyesetsa kuchita zinthu zofunika kwambiri komanso kugwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.

 • Muziyesa kuona zinthu m’njira yosiyanako. Ndi bwino kumakumbukira kuti zimene zingakudetseni nkhawa inuyo, munthu wina sizingamudetse nkhawa. Zimenezi zimachitika chifukwa anthufe timaona zinthu mosiyana. Taganizirani izi:

  1. Musamafulumire kukaikira zolinga za anthu ena. Mwachitsanzo, munthu akhoza kukulowererani pamzere. Ngati mutafulumira kuganiza kuti munthuyo ndi wamwano, mukhoza kukhumudwa. Koma m’malo moganizira zimenezo, ndi bwino kuganizira kuti mwina pali chinachake chomwe chamuchititsa.

  2. Muziona kuti zimene zikuchitikazo zikukupatsani mwayi wochita zinthu zina. Mwachitsanzo, ngati mukudikira dokotala kapena ngati mukudikira basi mukhoza kugwiritsa ntchito nthawi imeneyo powerenga kapena kuchita zinthu zina.

  3. Muziona patali. Mungadzifunse kuti, ‘Kodi likhaladi vuto lalikulu pofika mawa kapena mlungu wamawa?’ Muzisiyanitsa mavuto aakulu ndi aang’ono, otenga nthawi yaitali komanso yaifupi.

Muzichita Zinthu Mwadongosolo

“Koma zinthu zonse zizichitika moyenera ndi mwadongosolo.”​—1 AKORINTO 14:40.

Mfundo yake: Muziyesetsa kuchita zinthu mwadongosolo.

 • Tonsefe timasangalala zinthu zikamachitika mwadongosolo. Kuchita zinthu mozengereza ndi chinthu chimodzi chimene chimachititsa kuti zinthu zisamachitike molongosoka. Zimenezi zingachititse kuti ntchito yanu izingowunjikika ndipo pamapeto pake zingakuchititseni kukhala ndi nkhawa. Bwanji osayesa kuchita zinthu ziwiri zotsatirazi?

  1. Muzikonza ndandanda ya zinthu zomwe mukufuna kuchita n’kuyesetsa kuitsatira.

  2. Ganizirani chomwe chimachititsa kuti muzichita zinthu mozengereza n’kuyesetsa kusintha.

Musamangodzipanikiza ndi Ntchito

“Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwira ntchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.”​—MLALIKI 4:6.

Mfundo yake: Anthu ena amangogwira ntchito nthawi zonse. Anthu oterewa sapeza mpata wosangalala ndi ntchito yomwe agwira.

 • Muziona moyenera ntchito yanu komanso ndalama. Kukhala ndi ndalama zambiri sikupangitsa munthu kukhala wosangalala kapena kukhala ndi nkhawa zochepa. Lemba la Mlaliki 5:12 limati: “Zambiri zimene munthu wolemera amakhala nazo zimamulepheretsa kugona.” Choncho muziyesetsa kugwiritsa ntchito bwino ndalama zanu.

 • Muzipeza nthawi yopuma. Munthu amachepetsa nkhawa akamachita zinthu zimene amakonda. Komabe zosangalatsa zina zomwe munthu amachita atangokhala, monga kuonera TV, n’zosathandiza kwenikweni.

 • Musamangokhalira kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono. Mwachitsanzo, muzipewa kuona maimelo kapena mameseji pamalo ochezera a pa intaneti pokhapokha ngati pakufunikiradi kutero. Komanso musamawerenge ma imelo akuntchito pa nthawi yoti mwaweruka.

Muzisamalira Thanzi Lanu

“Kuchita masewera olimbitsa thupi n’kopindulitsa.”​—1 TIMOTEYO 4:8.

Mfundo yake: Kuchita masewera olimbitsa thupi nthawi zonse kungachititse kuti mukhale athanzi.

 • Muzikhala ndi zizolowezi zabwino. Kutakataka kungachititse kuti musamangokhala ndwii ndipo izi zingakuthandizeni kuti muchepetse nkhawa. Muzidya zakudya zopatsa thanzi komanso musamadzikhaulitse ndi njala. Muziyesetsa kupuma mokwanira.

 • Muzipewa njira zosathandiza zochepetsera nkhawa. Mwachitsanzo kumwa mowa mwauchidakwa, kusuta fodya komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. N’kupita kwa nthawi zinthu zimenezi zikhoza kungowonjezera nkhawa, kukuwonongerani thanzi komanso ndalama zanu.

 • Ngati mumakhala ndi nkhawa kwambiri, ndi bwino kukaonana ndi dokotala ndipo simuyenera kuchita manyazi kuchita zimenezi.

Muzichita Zinthu Zofunika Choyamba

“Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”​—AFILIPI 1:10.

Mfundo yake: Muziyamba ndi kuchita zinthu zofunika kwambiri.

 • Muzilemba zinthu zonse zomwe mukufuna kuchita mogwirizana ndi kufunika kwake. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti muyambe ndi ntchito zofunika kwambiri komanso mungadziwe ntchito zimene mukhoza kuzichita nthawi ina, kuzipereka kwa ena kapena kungozichotsa.

 • Mungayese kwa mlungu umodzi kuona mmene mukugwiritsira ntchito nthawi yanu. Kenako muziona zimene mungasinthe. Mukamachita zinthu zofunika pa nthawi yake, simungamapanikizike.

 • Muzikhala ndi nthawi yopuma. Ngakhale kupuma kanthawi kochepa, kungakuthandizeni kuti mupeze mphamvu komanso kuchepetsa nkhawa.

Muzipempha Ena Kuti Akuthandizeni

“Nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauweramitsa, koma mawu abwino ndi amene amausangalatsa.”​—MIYAMBO 12:25.

Mfundo yake: Mawu abwino komanso olimbikitsa angakuthandizeni kuti mumveko bwino.

 • Muzifotokozera nkhawa zanu munthu amene amakumvetsani. Mnzanu wapamtima angakuthandizeni kuti muyambe kuona zinthu moyenera ndipo nthawi zina akhozanso kukuthandizani kudziwa njira yothetsera vuto lanu. Komanso mukauza wina mavuto anu, zimathandiza kuti mupepukidwe.

 • Muzipempha thandizo. Mukhoza kugawirako ena ntchito kapena kuwapempha kuti akuthandizeni.

 • Ngati amene mumagwira naye ntchito wakukhumudwitsani, muzikambirana kuti muthetse nkhaniyo. Mwachitsanzo, mungamuuze mokoma mtima komanso mosamala mmene zochita zakezo zakukhudzirani. (Miyambo 17:27) Ngati zimenezi zalephereka, mungasankhe kusiya kuchitira naye limodzi zinthu zina.

Muzilola Kuti Mulungu Azikutsogolerani

“Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu, chifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo.”​—MATEYU 5:3.

Mfundo yake: Kuwonjezera pa chakudya, zovala komanso malo ogona, anthufe timafunikiranso kukwaniritsa zosowa zathu zauzimu. Choncho kuti tikhale osangalala timafunika kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu.

 • Pemphero ndi lofunika kwambiri. Mulungu amafuna kuti ‘muzimutulira nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’ (1 Petulo 5:7) Pemphero komanso kuganizira zinthu zabwino kungakuthandizeni kuti mukhale ndi mtendere wamumtima.​—Afilipi 4:6, 7.

 • Muziwerenga mabuku amene angakuthandizeni kuyandikira Mulungu. Mfundo zimene zafotokozedwa m’magaziniyi zachokera m’Baibulo ndipo zingakuthandizeni kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu. Zingakuthandizeninso kukhala ndi “nzeru zopindulitsa” komanso kuti mukhale ‘oganiza bwino.’ (Miyambo 3:21) Bwanji osakhala ndi cholinga choti muziwerenga Baibulo? Buku la Miyambo lingakhale poyambira pabwino.