Pitani ku nkhani yake

Moyo Wanthanzi

Moyo Wathanzi

Zimene Baibulo Limanena

Werengani kuti mudziwe zimene limanena pa nkhani ya matenda komanso chithandizo cha mankhwala.

Zimene Mungachite Kuti Mukhale Ndi Moyo Wathanzi

Werengani mfundo 5 zomwe zingakuthandizeni kuti mukhale ndi moyo wathanzi.

Kodi Tingapewe Bwanji Matenda?

Tsiku lililonse thupi lanu limamenya nkhondo yolimbana ndi adani osaoneka koma oopsa kwambiri.

N’zotheka Kumasangalalabe Ngakhale Muli Ndi Mavuto

Kodi mfundo za m’Baibulo zingakuthandizeni kuti muzisangalala?

Mtendere wa M’maganizo

Timakhala ndi mtendere wa m’maganizo tikamayesetsa kukhala odziletsa.

Mungatani Kuti Muzikhala Wosangalala​—Kukhala Wathanzi Komanso Wopirira

Kodi kuvutika ndi matenda kungachititse munthu kuti asamasangalale?

Samalani Kuti Musamapusitsike Ndi Nkhani Zabodza

Nkhani zosocheretsa, malipoti abodza ndi mphekesera zafala kwambiri ndipo zingakubweretsereni mavuto.

Ndingatani Kuti Ndichepetse Thupi?

Ngati mukufuna kuchepetsa thupi si bwino kumasala zakudya zina, mukhoza kungosintha zinthu zina pa moyo wanu.

Kodi Ndingatani Kuti Ndizidya Zakudya Zopatsa Thanzi?

Munthu amene sadya zakudya zopatsa thanzi ali wamng’ono amachitanso zomwezo akadzakula. Choncho ndibwino kuti muzikhala ndi chizolowezi chomadya zakudya zopatsa thanzi panopa.

Moyo Wathanzi

Mfundo za M’Baibulo zingatithandize kuti tizisamalira thanzi lathu.

Mungatani Kuti Muzisangalalabe Ngakhale Mutakalamba?

Werengani magaziniyi kuti mudziwe mfundo 6 zomwe zingakuthandizeni kuti muzisangalala ngakhale mutakalamba.

Kamphepo Kayaziyazi Komanso Dzuwa Ndi Mankhwala

Asayansi a makono apeza kuti zimene asayansi a m’zaka za 1800 anapeza n’zoona.

Kupirira Matenda

Zimene Zingakuthandizeni Ngati Mwayamba Kudwala Mwadzidzidzi

Kodi ndi mfundo ziti za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni ngati mwayamba kudwala mosayembekezereka?

Kodi Baibulo Lingandithandize Kupirira Matenda?

Inde. Onani mfundo zitatu zimene zingakuthandizeni kuti mupirire matenda.

Mmene Mungathandizire Amene Akudwala Matenda Amaganizo

Kuthandiza mnzanu yemwe akuvutika ndi matenda amaganizo kungasinthe zinthu pa moyo wake.

Kodi Pangakhale Chifukwa Chokhalira Ndi Moyo Ngati Tikudwala Matenda Aakulu?

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene zathandiza ena kupirira matenda aakulu.

Kodi Ndingatani Ngati Ndikudwala Matenda Aakulu? (Gawo 1)

Achinyamata 4 akufotokoza zimene zikuwathandiza kupirira matenda awo kuti asamangokhalira kudandaula.

Kodi Ndingatani Ngati Ndikudwala Matenda Aakulu?—Gawo 2

Werengani zimene achinyamata ena anachita kuti athe kupirira matenda aakulu komanso kuti azikhalabe osangalala.

Kodi Ndingatani Ngati Ndikudwala Matenda Aakulu?—Gawo 3

Zitsanzo za achinyamata atatu zingakuthandizeni kupirira matenda.

“Ndimayesetsa Kuti Ndisamangoganizira za Matenda Anga”

N’chiyani chimathandiza Elisa kupirira komanso kuiwalako matenda ake?

Kupirira Vuto la Kulumala

Mavuto Anga Andithandiza Kulimbitsa Ubwenzi Wanga Ndi Yehova

Mzimayi amene amayendera njinga ya olumala anapeza “mphamvu yoposa yachibadwa” chifukwa cha chikhulupiriro chake.

Amachita Zinthu Bwinobwino Ngakhale Kuti Ndi Osaona

Munthu akasiya kuona, ubongo wake umasintha n’kuyamba kugwiritsa ntchito ziwalo zina. Anthu osaona amadalira kwambiri kumva mawu, fungo komanso amadalira manja ndi zala zawo kuti adziwe zinthu

Jairo Amagwiritsa Ntchito Maso Ake Kutumikira Mulungu

Jairo amadwala matenda a muubongo oopsa kwambiri komabe amaona kuti moyo wake ndi waphindu.

Kutumikira Mulungu Kuli Ngati Mankhwala Ake

Onesmus anabadwa ndi matenda a mafupa. Onani mmene malonjezo a m’Baibulo amulimbikitsira

Wosaona Ndiponso Wosamva

James Ryan anabadwa ndi vuto losamva ndipo kenako anakhalanso ndi vuto losaona. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kudziwa cholinga cha moyo?

Kavidiyo: “Kaya Ndikanagwira Mtengo Wanji?”

Onerani kavidiyoka kuti mumve zimene munthu wina wakhungu ananena poyamikira mmene Baibulo la zilembo za akhungu lamuthandizira.

Yehova Wandichitira Zazikulu

Félix Alarcón anaona kuti moyo wake uli ndi tsogolo labwino pambuyo pa ngozi ya njinga yamoto yomwe inapangitsa kuti afe ziwalo kuchokera khosi kupita m’munsi.

Yehova Anandithandiza pa Nthawi Yomwe Ndinkafunikiradi Kuthandizidwa

Ali ndi zaka 20, Miklós Aleksza analumala atachita ngozi. Kodi Baibulo linamuthandiza bwanji kukhala ndi chiyembekezo?

Kusamalira Ena

Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yosamalira Makolo Achikulire?

Baibulo limafotokoza zimene amuna ndi akazi ena anachita m’mbuyomo posamalira makolo awo achikulire. Lilinso ndi mfundo zomwe zingathandize anthu omwe akusamalira makolo achikulire panopa.

Zimene Mungachite Ngati Muli ndi Mwana Wolumala

Werengani kuti mumve za mavuto atatu amene mwina mumakumana nawo komanso mmene Baibulo lingakuthandizireni.

Kodi Ndingatani Ngati Bambo Kapena Mayi Anga Atayamba Kudwala?

Si inu nokha amene mukukumana ndi vuto limeneli. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene atsikana ena awiri anachita kuti athe kupirira.

Mungatani Ngati Munthu Amene Mumamukonda Akudwala Matenda Oti Sachira?

Kodi achibale angalimbikitse komanso kusamalira bwanji munthu amene akudwala matenda oti sachira? Kodi achibale angatani kuti asavutike kwambiri pa nthawi imene m’bale wawoyo akudwala?

Matenda

Zimene Muyenera Kudziwa Zokhudza Matenda a Muubongo

Zinthu 9 zomwe zingakuthandizeni ngati mukudwala matenda a muubongo.

Zimene Mungachite Kuti Mupewe Matenda a Shuga

Anthu 90 pa 100 alionse amene ali ndi shuga wopitirira mlingo woyenera sadziwa zimenezi.

Zimene Muyenera Kudziwa Ponena za Matenda a Khunyu

Anthu ambiri sawamvetsa matenda a khunyu. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zinthu zina zomwe muyenera kudziwa ponena za matendawa

Zimene Mungachite Kuti Mupewe Matenda a Chiseyeye

Chiseyeye ndi amodzi mwa matenda ofala kwambiri padziko lonse. Kodi n’chiyani chimayambitsa matendawa? Kodi mungadziwe bwanji kuti mukudwala matendawa? Kodi mungatani kuti musadwale matendawa.

Kodi Kudana ndi Kusagwirizana ndi Zakudya kwa Thupi N’kosiyana Bwanji?

Kodi kungoganiza kuti muli ndi vuto n’kuthamangira kusiya zakudya zinazake kuli ndi mavuto otani?

Kodi Mukudziwa Zotani pa Nkhani ya Malungo?

Mukhoza kudziteteza ngati mumakhala kapena mukupita kudziko limene kuli malungo.

Kupirira Mavuto Amene Azimayi Amakumana Nawo Akamasiya Kusamba

Ngati inuyo komanso mwamuna wanu mutamvetsa zimene zimachitika munthu akamasiya kusamba, mudzatha kupirira mosavuta mavuto omwe amachitika.

Kuvutika Maganizo

Zimene Baibulo Limanena Pa Nkhani ya Kuvutika Maganizo

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe chifukwa chake anthu amadwala matenda ovutika maganizo komanso mmene Baibulo lingawathandizire.

Kodi Kudzipha Ndi Njira Yabwino Yothetsera Mavuto

N’chiyani chingachititse munthu kumaona kuti imfa si mdani?

Mukamaona Kuti Simungathenso Kupirira

Ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto, pali chifukwa chokhalira ndi moyo.

N’chifukwa Chiyani Achinyamata Ambiri Akudwala Matenda Ovutika Maganizo?

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zizindikiro zake ndiponso zimene zimayambitsa matendawa. Onani zimene makolo komanso anthu ena angachite kuti athandize achinyamatawa.

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangoganizira Zinthu Zolakwika?

Mukhoza kumaganizira zinthu zabwino mukamatsatira mfundo zomwe zili mu nkhaniyi.

Achinyamata Ambiri Akuvutika Ndi Matenda Amaganizo—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Baibulo limapereka malangizo othandiza kwa achinyamata omwe akuvutika maganizo.

N’chifukwa Chiyani Ndimadzivulaza?

Achinyamata ena ali ndi vuto lodzivulaza mwadala. Ngati muli ndi khalidwe limeneli, kodi mungatani kuti mulisiye?

Kodi Ndingatani Ngati Ndili ndi Matenda Ovutika Maganizo?

Mfundo zomwe zili m’nkhaniyi zingakuthandizeni kudziwa zimene mungachite kuti muchire.

Kodi Baibulo Lingandithandize Ngati Ndili ndi Nkhawa?

Pali zinthu zitatu zimene Mulungu amapereka kuti athandize anthu amene ali ndi nkhawa.

Kodi Baibulo Lingandithandize Ngati Ndili ndi Maganizo Ofuna Kudzipha?

Kodi Baibulo limapereka malangizo otani kwa munthu amene akufuna kudzipha?

Nkhawa

Kodi Tingatani Kuti Tisamade Nkhawa Kwambiri?

Kodi ndi mavesi a m’Baibulo ati komanso zinthu ziti zimene zingakuthandizeni kuti musamade nkhawa kwambiri?

Baibulo Lingathandize Amuna Amene Ali Ndi Nkhawa

Nkhawa ndi vuto lalikulu kwambiri popeza tili munthawi yapadera komanso yovuta, ndiye kodi Baibulo lingakuthandizeni?

Zimene Mungachite Ngati Muli Nokhanokha

Mukamamva kuti muli nokhanokha, mungayambe kuona kuti simungathe kupeza chiyembekezo, chimwemwe komanso kukhala wokhutira​—komatu si choncho.

Zimene Zingatithandize Ngati Tatopa ndi Mliri

Ngati sitichita zinthu zimene zingatithandize kuti tisatope ndi mliriwu, pang’ono ndi pang’ono tingayambe kugwa ulesi pa nkhani yotsatira malangizo otitetezera ku COVID-19.

Mungatani Kuti Muchepetse Nkhawa?

Onani njira zomwe mungatsatire kuti musamakhale ndi nkhawa kapena kuti mukwanitse kuzichepetsa.

N’chiyani Chingandithandize Ndikakhala Ndi Nkhawa?

Zinthu 5 zimene zingakuthandizeni kuti muzida nkhawa pa zinthu zoyenera m’malo mwa zinthu zimene zingakubweretserani mavuto.

Kodi Baibulo Lingakuthandizeni Mukakhala Ndi Nkhawa?

Nkhawa ndi mbali imodzi ya moyo wa munthu. Kodi n’zotheka kukhala opanda nkhawa?

Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani ya Nkhawa

Nkhawa zothandiza ndi zabwino; nkhawa zoipa zimatibweretsera mavuto. Kodi mungatani kuti nkhawa zisamakulepheretseni kukhala osangalala?

Kodi Mungatani Ngati Mukuvutika Maganizo?

Malangizo a m’Baibulo angakuthandizeni kuthana ndi kuvutika maganizo komwe nthawi zambiri kumayamba ndi zinthu 4.

Vuto Limene Limakhalapo: Kupanikizika

Mukamayesa kuchita zonse nokha mukhoza kulephera kuchita chilichonse. Kodi mungatani kuti musamapanikizike?

Kodi Ineyo Ndingatani Kuti Ndipewe Vuto la Kupanikizika?

Kodi n’chiyani chimayambitsa vuto la kupanikizika? Kodi inunso mumapanikizika kwambiri? Ngati ndi choncho, kodi mungatani kuti muthane ndi vutoli?

Ngati Mwana Wanu Wamkazi Akuvutika Maganizo

Atsikana ambiri amavutika ndi zimene zimachitika akamakula. Kodi makolo angawathandize bwanji akamavutika maganizo chifukwa cha zimenezi?

Kodi Ndimafuna Kuti Ndisamalakwitse Chilichonse?

Kodi mungasiyanitse bwanji pakati pa kuyesetsa kuchita bwino ndi kuyesa kuchita zinthu zosatheka?

Zimene Mungachite Zinthu Zikasintha

Zinthu zimasintha pamoyo. Onani zimene ena achita kuti azolowere zinthu zitawasinthira.

N’chiyani Chingakuthandizeni Kuti Musamakhale Mwamantha?

Mfundo zitatu zothandiza kuti musamadzione ngati wosafunika.

Chithandizo cha Mankhwala

Kodi Mkhristu Angalandire Chithandizo cha Mankhwala Akadwala?

Kodi chithandizo chimene tingasankhe chimakhudza ubwenzi wathu ndi Mulungu?

Kodi Mungathandize Bwanji Mnzanu Kapena Wachibale Akadwala?

Anthu ambiri amada nkhawa akauzidwa kuti agonekedwa m’chipatala kapena azipita kukaonana ndi dokotala. Kodi mungathandize bwanji mnzanu kapena wachibale akadwala?

Zimene Madokotala Akunena Masiku Ano pa Nkhani Yoika Magazi Anthu Odwala

Anthu akhala akunyoza a Mboni za Yehova chifukwa chokana kuikidwa magazi. Kodi madokotala ena akunena zotani pa nkhaniyi?