Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZOPEREKA ZANU ZIMAGWIRITSIDWA NTCHITO BWANJI?

Kuchita Misonkhano ya Mpingo pa Vidiyokomfelensi

Kuchita Misonkhano ya Mpingo pa Vidiyokomfelensi

26 JUNE, 2020

 Mayiko ambiri padziko lonse alamula kuti anthu azikhala motalikirana ndipo sakulola kuti azisonkhana pamodzi. A Mboni za Yehova akuyesetsa kumvera lamuloli komabe iwo akupitiriza kuchita misonkhano yawo. Pofuna kukhala otetezeka, mipingo ina ikumachita misonkhano pa Vidiyokomfelensi ndipo ikumagwiritsa ntchito mapulogalamu ngati Zoom.

 Kuti tizichita misonkhano mlungu uliwonse, Bungwe Lolamulira linavomereza kuti zopereka zathu zizigwiritsidwa ntchito polipirira pulogalamu ya Zoom yoti mipingo izigwiritsa ntchito. Zimenezi zathandiza kwambiri mipingo yomwe sikanakwanitsa kulipira pulogalamuyi pa mtengo wa madola 15 mpaka 20 kapena kuposerapo. Poyamba mipingoyi inkagwiritsa ntchito mapulogalamu aulere omwe sankalola kulumikiza anthu ambiri komanso sanali otetezeka mokwanira. Koma panopa mipingo yonse imene imagwiritsa ntchito pulogalamu ya Zoom yomwe gulu limalipirayi, imatha kulumikiza anthu ambiri m’njira yotetezeka komanso mosavuta. Pofika pano, mipingo yoposa 65,000 m’mayiko oposa 170 ikugwiritsa ntchito pulogalamu imeneyi.

 Mpingo wa Kairagi womwe uli m’tawuni ya Manado ku North Sulawesi m’dziko la Indonesia, unasiya kugwiritsa ntchito pulogalamu ina yaulere ndipo unayamba kugwiritsa ntchito pulogalamu ya Zoom yomwe gulu limalipira. M’bale Hadi Santoso anafotokoza kuti: “Ngakhale abale ndi alongo omwe sanazolowere kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono, amatha kuchita nawo misonkhanoyi mosavuta chifukwa safunika kulowa mobwerezabwereza kuti amvetsere nawo msonkhano.”

 M’bale wina dzina lake Lester Jijón, Jr., yemwe ndi mkulu mumpingo wa Guayacanes Oeste ku Guayaquil m’dziko la Ecuador, ananena kuti: “Chifukwa choti abale ndi alongo ambiri ndi osauka, zikanakhala zovuta kuti mipingo ina izitha kulipira yapulogalamu Zoom kuti anthu onse mumpingo azitha kuchita misonkhano pamodzi. Koma panopa, chifukwa choti tikugwiritsa ntchito pulogalamuyi timatha kulumikiza anthu ambiri ndiponso zimakhala zosavuta kuti tiitanire anthu ena kuti achite nawo misonkhano.”

 M’bale wina dzina lake Johnson Mwanza, yemwe ndi mkulu mumpingo wa Ngwerere North mumzinda wa Lusaka ku Zambia, analemba kuti: “Abale ndi alongo ambiri akhala akunena mobwerezabwereza kuti kuchita misonkhano pa vidiyokomfelensi kukutithandiza kuona kuti tili pafupi kwambiri ndi abale ndi alongo athu ndiponso tikuona kuti Yehova amatikonda kwambiri komanso akutisamalira.’”

 Gulu limalipira pulogalamuyi pogwiritsa ntchito ndalama zimene zimaperekedwa kuti zizithandiza pakachitika masoka a chilengedwe. Ndalamazi zimachokera pa zopereka zaufulu zothandiza pa ntchito yapadziko lonse. Zambiri mwa ndalamazi zimaperekedwa kudzera pa donate.jw.org. Tikukuyamikirani kwambiri chifukwa cha zopereka zanu zomwe zimathandizanso pakachitika masoka achilengedwe padziko lonse.—2 Akorinto 8:14.