Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zipembedzo Ziyenera Kuchita Nawo Zandale?

Kodi Zipembedzo Ziyenera Kuchita Nawo Zandale?

 Padziko lonse, anthu omwe amati ndi otsatira a Yesu Khristu amalowerera kwambiri munkhani zandale. Zipembedzo zina zimauza anthu kuti akavotere munthu kapena chipani chinachake ndi cholinga chofuna kulimbikitsa mfundo ndi miyambo yachipembedzocho. Chifukwa cha zimenezi, andale nawonso, nthawi zambiri amalankhula za kufunika kokhala ndi makhalidwe abwino ndi cholinga chofuna kukopa anthu azipembedzo zosiyanasiyana kuti akhale kumbali yawo. Ndipo sizachilendo kuona atsogoleri achipembedzo akupikisana nawo pazisankho. M’mayiko ena, chipembedzo chachikhristu chimakhala ndi mphamvu zambiri ndipo mwina chimadziwika monga chipembedzo cha dzikolo.

 Inuyo mukuganiza bwanji? Kodi otsatira a Yesu ayenera kuchita nawo zandale? Tikhoza kupeza yankho la funsoli tikaganizira chitsanzo chimene Yesu anasonyeza. Iye anati: “Pakuti ndakupatsani chitsanzo kuti mmene ine ndachitira kwa inu, inunso muzichita chimodzimodzi.” (Yohane 13:15) Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani pa nkhani yochita zandale?

Kodi Yesu ankachita nawo zandale?

 Ayi. Yesu sankalowerera nawo nkhani zandale.

 Yesu sankafuna udindo pa nkhani zandale. Satana atanena kuti amupatsa “maufumu onse a padziko,” Yesu sanavomere kuti apatsidwe udindo wokhala wolamulira padzikoli. (Mateyu 4:8-10) a Komanso anthu ena omwe ankaona kuti Yesu angakhale mtsogoleri wabwino, ankafuna kuti Yesu azichita nawo zandale. Koma Baibulo limanena kuti: “Yesu atadziwa kuti iwo akufuna kumugwira kuti amuveke ufumu, anachoka ndi kupitanso kuphiri yekhayekha.” (Yohane 6:15) Yesu sanavomere kuchita zomwe anthuwo ankafuna. M’malomwake, iye anakana kulowerera munkhani zandale.

 Yesu sankatenga nawo mbali iliyonse pa nkhani zandale. Mwachitsanzo, Ayuda a munthawi ya Yesu sankasangalala ndi zoti azipereka msonkho ku boma la Roma ndipo ankaona kuti akuponderezedwa. Nthawi ina anthuwo ankafuna kumva maganizo a Yesu ngati zinalidi zoyenera kuti azipereka msonkhowo koma Yesu sanafune kukambirana nawo chilichonse chokhudza ndale. M’malomwake anawauza kuti: “Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma zinthu za Mulungu muzizipereka kwa Mulungu.” (Maliko 12:13-17) Yesu sanafune kutenga nawo mbali pamikangano yandale. Koma iye anasonyeza kuti msonkho womwe akuluakulu a boma la Roma (omwe ankaimira Kaisara) ankafuna, unayenera kuperekedwa. Zomwe Yesu analankhula panthawiyi, zinasonyezanso kuti sitiyenera kumangomvera chilichonse chomwe olamulira anena. Munthu sayenera kupereka ku Boma zinthu zomwe ndi zoyenera kuperekedwa kwa Mulungu. Zinthu ngati kudzipereka komanso kulambira, ndi zoyenera kupita kwa Mulungu yekha.—Mateyu 4:10; 22:37, 38.

 Yesu ankalimbikitsa anthu kukhala kumbali ya Ufumu wa Mulungu womwe ndi boma lakumwamba. (Luka 4:43) Iye sankachita nawo zandale chifukwa ankadziwa kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha, osati maboma a anthu, womwe ungadzachititse dzikoli kukhala malo abwino ngati mmene Mulungu amafunira. (Mateyu 6:10) Iye ankadziwa kuti Ufumu wa Mulungu sudzalamulira pogwiritsa ntchito maulamuliro a anthu. Koma kuti udzalowa m’malo mwa maboma a anthuwo.—Danieli 2:44.

Kodi Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankachita nawo zandale?

 Ayi. Iwo ankatsatira lamulo la Yesu lomwe anawalamula kuti “simuli mbali ya dzikoli.” (Yohane 15:19) Ophunzirawa, ankatsanzira chitsanzo chake ndipo sankalowerera nawo munkhani za ndale. (Yohane 17:16; 18:36) M’malo molowerera nawo munkhanizi, iwo ankagwira ntchito yomwe Yesu anawalamula, yolalikira ndi kuphunzitsa anthu za Ufumu wa Mulungu,.—Mateyu 28:18-20; Machitidwe 10:42.

 Akhristuwa ankaona kuti kumvera Mulungu kuyenera kukhala pamalo oyamba. Komabe ankadziwa kuti afunika kumvera akuluakulu aboma. (Machitidwe 5:29; 1 Petulo 2:13, 17) Iwo ankamvera malamulo komanso kulipira misonkho. (Aroma 13:1, 7) Ngakhale kuti sankatenga nawo mbali iliyonse munkhani zandale, ankadalira malamulo aboma kuti atetezeke. Komanso ankadalira zinthu zina zofunika zomwe boma linkapereka.—Machitidwe 25:10, 11; Afilipi 1:7.

Akhristu a masiku ano sachita nawo zandale

 Baibulo limasonyeza kuti Yesu ndi ophunzira ake sankalowerera nkhani zandale. Chifukwa cha zimenezi Akhristu a Mboni za Yehova padziko lonse, nawonso satenga nawo mbali iliyonse pa nkhani zandale. Mofanana ndi Akhristu oyambirira, nawonso amagwira ntchito imene Yesu analamula, yolalikira “uthenga wabwino uwu wa Ufumu.”—Mateyu 24:14.

a Ngakhale kuti Yesu anakana kupatsidwa ulamuliro, iye sanatsutse zoti maulamuliro a padzikoli ndi a Satana. Ndipo pambuyo pake anatchula Satana kuti “wolamulira wa dziko.”—Yohane 14:30.