Pitani ku nkhani yake

Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Chiyani?

Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Chiyani?

Yankho la m’Baibulo

Ufumu wa Mulungu udzathetsa maboma onse a anthu ndipo Ufumu wokhawo ndi womwe uzidzalamulira dziko lonse lapansi. (Danieli 2:44 Chivumbulutso 16:14) Zimenezi zikadzachitika, Ufumu wa Mulungu udzachita zotsatirazi:

  • Udzawononga anthu onse oipa, omwe amachita zinthu modzikonda n’kumasowetsa mtendere ena tonsefe. Baibulo limati: “Oipa adzachotsedwa padziko lapansi.”—Miyambo 2:22.

  • Udzathetsa nkhondo zonse. Baibulo limati: “[Mulungu] akuletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”—Salimo 46:9.

  • Udzathandiza anthu kukhala osangalala komanso otetezeka. Baibulo limati: “Aliyense adzakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu ndipo sipadzakhala wowaopsa.”—Mika 4:4.

  • Udzachititsa dzikoli kukhala paradaiso. Baibulo limati: “Chipululu ndi malo opanda madzi zidzasangalala. Dera lachipululu lidzakondwa ndipo lidzachita maluwa n’kukhala lokongola ngati duwa la safironi.”—Yesaya 35:1.

  • Udzathandiza munthu aliyense kuti azidzagwira ntchito yabwino komanso yosangalatsa. Baibulo limati: “Ndipo anthu anga [a Mulungu] osankhidwa mwapadera adzapindula mokwanira ndi ntchito ya manja awo. Sadzagwira ntchito pachabe.”—Yesaya 65:21-23.

  • Udzathetsa matenda. Baibulo limati: “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”—Yesaya 33:24.

  • Udzachititsa kuti anthufe tisamadzakalambe. Baibulo limati: “Mnofu wake usalale kuposa mmene unalili ali mnyamata. Abwerere ku masiku ake aunyamata pamene anali ndi mphamvu.”—Yobu 33:25.

  • Akufa adzaukitsidwa. Baibulo limati: “Onse ali m’manda achikumbutso adzamva mawu [a Yesu] ndipo adzatuluka.”—Yohane 5:28, 29.