Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zidindo Zakale Zinkagwira Ntchito Yanji?

Kodi Zidindo Zakale Zinkagwira Ntchito Yanji?

Zidindo zinali zipangizo zimene ankazigwiritsa ntchito podinda zinthu ndipo nthawi zambiri ankadinda padongo lofewa kapena pa zinthu zaphalaphala zomwe ankazigwiritsa ntchito pomatira. Zidindozi zinkaoneka mosiyanasiyana, zina zinali zozungulira, zina zinali za makona 4 ndipo zina zinkaoneka ngati mitu ya zinyama. Chidindo chinkasonyeza mwiniwake wa chinthu komanso chinkapereka umboni wotsimikizira kuti chikalata chomwe chalembedwa ndi chenicheni. Anthu ankaikanso chidindo pa zikwama zawo kapenanso pa zinthu zina, monga pa zitseko kapenanso pakhomo lolowera kumanda pofuna kuti zitetezedwe.

Chidindo chozungulira chosonyeza Dariyo 1 mfumu ya Perisiya akusaka nyama komanso chidindo chodindidwa padongo lofewa

Anthu ankapanga zidindo pogwiritsa ntchito zinthu zosiyanasiyana monga mafupa, miyala ya laimu, miyala ya mitundu ina yosiyanasiyana, zitsulo kapenanso matabwa. Nthawi zina pa zidindozi pankalembedwa dzina la mwini chidindocho komanso la bambo ake. Zidindo zina zinkasonyezanso udindo womwe munthuyo ali nawo.

Pofuna kutsimikizira kuti chikalata chimene chalembedwa ndi chenicheni, mwiniwake wa chidindo ankadinda chizindikiro chake padongo lofewa kapena zinthu zaphalaphala ndipo ankazimata pa chikalatacho. (Yobu 38:14) Pakapita nthawi, zomatirazo zinkauma ndipo zinkachititsa kuti chikalatacho chikhale chotetezeka komanso kuti chisasinthidwe.

Zidindo Zinkagwiritsidwanso Ntchito Popereka Udindo M’manja mwa Munthu Wina

Munthu akafuna kupereka udindo wake kwa munthu wina, ankamupatsa chidindo chake. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene zinachitika pakati pa Farao wa ku Iguputo ndi Yosefe mwana wa Yakobo, yemwe anali Mheberi. Yosefe anali kapolo ku Iguputo ndipo kenako anamangidwa mopanda chilungamo. Patapita nthawi, Farao anamutulutsa m’ndende ndipo anamukweza udindo kuti akhale nduna yaikulu. Baibulo limanena kuti: “Atatero, Farao anavula mphete yake yachifumu kudzanja lake, n’kuiveka kudzanja la Yosefe.” (Genesis 41:42) Popeza kuti mpheteyo inali ndi chidindo chosonyeza udindo wa Farao, zimenezi zinasonyeza kuti Yosefe wapatsidwa udindo komanso mphamvu yogwirira ntchito imene anapatsidwa.

Mfumukazi Yezebeli wa ku Isiraeli anagwiritsa ntchito chidindo cha mwamuna wake pokonza chiwembu choti aphe Naboti. Iye analemba makalata m’dzina la Mfumu Ahabu opempha akulu ena kuti aphe Naboti yemwe anali osalakwa, pomunamizira kuti wanyoza Mulungu. Yezebeli anadinda chidindo cha mfumu pa makalatawo ndipo chiwembucho chinathekadi.—1 Mafumu 21:5-14.

Mfumu Ahasiwero ya ku Perisiya inadinda makalata ndi mphete yake yodindira pofuna kutsimikizira kuti makalatawo anali enieni.—Esitere 3:10, 12.

Nehemiya, amene analemba nawo Baibulo ananena kuti akalonga a ku Isiraeli, Alevi komanso ansembe akafuna kuvomereza pangano lomwe lachita kulembedwa, ankadinda chidindo.—Nehemiya 1:1; 9:38.

Baibulo limatchula za nthawi ziwiri zomwe chidindo chinagwiritsidwa ntchito poteteza malo olowera. Pa nthawi imene mneneri Danieli anaponyedwa m’dzenje la mikango, anthu “anabweretsa mwala ndi kutseka pakhomo la dzenjelo.” Kenako Mfumu Dariyo, yomwe inkalamulira Mediya ndi Perisiya, “inadinda mwalawo ndi mphete yake yodindira ndipo nduna zakenso zinaudinda ndi mphete yawo yodindira, kuti chilichonse chokhudza Danieli chisasinthidwe.”—Danieli 6:17.

Thupi la Yesu Khristu litaikidwa m’manda, adani ake ‘anakakhwimitsa chitetezo pamandawo potseka kwambiri mandawo ndi chimwala’ chomwe anatsekera khomo lolowera. (Mateyu 27:66) N’kutheka kuti amene anakhwimitsa chitetezowo anali ena mwa akuluakulu a boma. Ndipo ngati zinalidi choncho, buku lina lolembedwa ndi David L. Turner, lofotokoza za buku la m’Baibulo la Mateyu linanena kuti anthuwo, “ayenera kuti anagwiritsa ntchito chidindo chomwe anachidinda padongo kapena zinthu za phalaphala zomwe zinamatidwa potseka mng’alu womwe unali pakati pa . . . chimwalacho ndi khomo lolowera kumandawo.”

Tikhoza kuphunzira zambiri tikaona mmene zidindo zakale zinkagwirira ntchito. N’chifukwa chake akatswiri ofufuza zinthu zakale komanso olemba mbiri akufunitsitsa atadziwa zambiri zokhudza zidindozi. Ndipotu cholinga chachikulu cha kafukufuku yemwe akuchita panopa ndi kufufuza zokhudza zidindo zakale.