Pitani ku nkhani yake

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Yohane 3:16​—“Mulungu Anakonda Kwambiri Dziko”

Yohane 3:16​—“Mulungu Anakonda Kwambiri Dziko”

“Pakuti Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”—Yohane 3:16, Baibulo la Dziko Latsopano.

“Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero kuti anapatsa Mwana wace wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike koma akhale nao moyo wosatha.”—Yohane 3:16, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Yohane 3:16

Mulungu amatikonda kwambiri ndipo amafuna kuti tidzapeze moyo wosatha. Choncho anatumiza Mwana wake Yesu Khristu kuti abwere padzikoli. Yesu ali padzikoli anachita zinthu zambiri. Mwachitsanzo, anauza otsatira ake za Mulungu yemwe ndi Atate wake. (1 Petulo 1:3) Iye anaperekanso moyo wake kuti apulumutse anthu. Kuti tikhale ndi moyo wosatha, tiyenera kukhulupirira Yesu.

Mawu akuti “anapereka Mwana wake wobadwa yekha” a amasonyeza kuti Mulungu amakonda kwambiri anthu. Yesu ndi Mwana wapadera kwambiri wa Mulungu. N’chifukwa chiyani tikutero? Yesu yekha ndi amene analengedwa mwachindunji ndi Mulungu. (Akolose 1:17) Iye ndi “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.” (Akolose 1:15) Kenako Mulungu anagwiritsa ntchito Yesu polenga angelo komanso zinthu zina zonse. Ndiye Yehova b Mulungu anapereka ndi mtima wonse Mwana wake wokondedwayu ‘kudzatumikira anthu komanso kupereka moyo wake ngati dipo kuti awombole anthu ambiri.’ (Mateyu 20:28) Anthufe tinatengera uchimo kwa Adamu, ndiyeno Yesu anavutika mpaka kuphedwa kuti atipulumutse ku uchimo ndi imfa.​—Aroma 5:8, 12.

Kukhulupirira Yesu kumatanthauza zambiri osati kungokhulupirira zoti alipo komanso kuti anatichitira zazikulu. Tingasonyeze kuti timakhulupirira Mwana wa Mulungu ngati timamumvera komanso kutsatira mapazi ake. (Mateyu 7:24-27; 1 Petulo 2:21) Baibulo limanena kuti: “Iye wokhulupirira mwa Mwanayo ali nawo moyo wosatha. Wosamvera Mwanayo sadzauona moyowu.”—Yohane 3:36.

Nkhani Yonse Yokhudza Yohane 3:16

Yesu ananena mawuwa polankhula ndi mtsogoleri wachipembedzo chachiyuda dzina lake Nikodemo. (Yohane 3:1, 2) Pamene ankakambirana naye, Yesu anafotokoza za Ufumu wa Mulungu c komanso “kubadwanso.” (Yohane 3:3) Anafotokozanso za imfa yake. Anati: “Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa m’mwamba [kupachikidwa pa mtengo], kuti aliyense wokhulupirira iye akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:14, 15) Ndiyeno anatsindika mfundo yakuti mwayi wodzapeza moyowu ukutheka chifukwa chakuti Mulungu amakonda kwambiri anthu. Yesu anamaliza pofotokoza kuti munthu angadzapeze moyowu ngati ali ndi chikhulupiriro komanso amachita zinthu zosangalatsa Mulungu.—Yohane 3:17-21.

a Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “wobadwa yekha” amatanthauza “wamtundu wapadera kapena kuti mmodzi yekhayo, ndipo palibenso wina wofanana ndi ameneyo kapena wamtundu umenewo.”—A Greek-English Lexicon of the New Testament and Other Early Christian Literature, tsa. 658

b Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu.—Salimo 83:18.

c Ufumu wa Mulungu umatchedwanso “Ufumu wakumwamba” chifukwa choti ndi boma lakumwambako. (Mateyu 10:7; Chivumbulutso 11:15) Mulungu anasankha Khristu kuti akhale Mfumu ya Ufumu umenewu. Ufumu wa Mulungu udzachititsa kuti cholinga cha Mulungu polenga dzikoli chitheke. (Danieli 2:44; Mateyu 6:10) Kuti mumve zambiri onani nkhani yakuti “Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?