Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NSANJA YA OLONDA Na. 1 2024 | Kodi Tingapeze Kuti Malangizo Otithandiza Kusankha Zinthu Mwanzeru?

Kodi mumasankha bwanji pakati pa zoyenera ndi zosayenera? Anthu ambiri amasankha zinthu potengera zimene chikumbumtima chawo chikuwauza kapenanso zimene anaphunzira kwa anthu ena. Pomwe ena amasankha zinthu potengera maganizo a anthu ena. Nanga inuyo n’chiyani chimakuthandizani kusankha pakati pa zoyenera ndi zosayenera? Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kutsimikizira kuti zimene mungasankhe panopa zidzathandiza kwambiri inuyo komanso anthu a m’banja lanu?

 

Tonsefe Tili Ndi Udindo Wosankha Choyenera Ndi Chosayenera

Kodi mudzafufuza kuti malangizo okuthandizani kusankha zoyenera kuchita pa nkhani ya makhalidwe abwino?

Kodi Anthu Ambiri Amasankha Bwanji Pakati pa Choyenera ndi Chosayenera?

Tingasankhe zochita pa nkhani ya choyenera ndi chosayenera potengera mmene tikumvera kapenanso mmene anthu ena angationere. Koma kodi pali njira ina yodalirika?

Tizikhulupirira Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani ya Zoyenera Ndi Zosayenera

Kodi mungatsimikizire bwanji kuti Baibulo lili ndi malangizo othandiza kusankha zoyenera pa nkhani ya makhalidwe abwino?

Malangizo a M’Baibulo Okhudza Zoyenera Ndi Zosayenera Ndi Othandiza

Onani mmene kutsatira malangizo a m’Baibulo kwathandizira anthu mamiliyoni ambirimbiri pa mbali 4 za moyo wawo.

Kodi Malangizo Odalirika Mungawapeze Kuti?

Baibulo lingakuthandizeni kusankha zinthu mwanzeru.