Pitani ku nkhani yake

Kodi Mipingo Yanu Imayendetsedwa Bwanji?

Kodi Mipingo Yanu Imayendetsedwa Bwanji?

Mpingo uliwonse umayendetsedwa ndi bungwe la akulu. Mipingo pafupifupi 20 imapanga dera ndipo madera pafupifupi 10 amapanga chigawo. Nthawi ndi nthawi, mpingo uliwonse umachezeredwa ndi akulu ena amene amayendera mipingo, omwe timawatchula kuti oyang’anira madera ndiponso oyang’anira zigawo.

Mipingo imalandira malangizo a m’Baibulo ochokera ku Bungwe Lolamulira. Bungweli lapangidwa ndi a Mboni amene atumikira Mulungu kwa nthawi yaitali, omwe panopa ali kumaofesi a Mboni za Yehova a ku Brooklyn, mumzinda wa New York ku America. Maofesi amenewa ndi likulu la Mboni za Yehova padziko lonse.—Machitidwe 15:23-29; 1 Timoteyo 3:1-7.