Salimo 26:1-12
Salimo la Davide.
26 Ndiweruzeni,+ inu Yehova, pakuti ine ndayenda mogwirizana ndi mtima wanga wosagawanika,+Ndipo ndikudalira Yehova kuti ndisagwedezeke.+
2 Ndisanthuleni, inu Yehova, ndi kundiyesa.+Yengani impso zanga ndi mtima wanga.+
3 Pakuti kukoma mtima kwanu kosatha kuli pamaso panga.Ine ndayenda m’choonadi chanu.+
4 Sindinakhale pansi pamodzi ndi anthu achinyengo.+Ndipo sindinayanjane ndi anthu obisa umunthu wawo.+
5 Ndimadana ndi mpingo wa anthu ochita zoipa,+Ndipo sindikhala pansi ndi anthu oipa.+
6 Ndidzasamba m’manja mwanga kusonyeza kuti ndine wopanda cholakwa,+Ndipo ndidzayenda mozungulira guwa lanu lansembe, inu Yehova,+
7 Kuti mawu anga oyamikira amveke kwambiri,+Ndi kulengeza ntchito zanu zonse zodabwitsa.+
8 Yehova, ine ndimakonda nyumba imene inu mumakhala+Ndi malo amene kumakhala ulemerero wanu.+
9 Musachotse moyo wanga pamodzi ndi anthu ochimwa,+Kapena pamodzi ndi anthu a mlandu wamagazi.+
10 M’manja mwa anthu amenewa muli khalidwe lotayirira,+Ndipo m’dzanja lawo lamanja mwadzaza ziphuphu.+
11 Koma ine ndidzayenda mogwirizana ndi mtima wanga wosagawanika.+Ndiwomboleni+ ndi kundikomera mtima.+
12 Phazi langa lidzaimadi pamalo athyathyathya.+Pamsonkhano, ndidzatamanda Yehova.+