Salimo 13:1-6

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide. 13  Kodi mudzandiiwala kufikira liti, inu Yehova?+ Mpaka muyaya?+Mudzandibisira nkhope yanu kufikira liti?+   Kodi ndidzalimbana ndi masautso anga kufikira liti?Kodi masiku a moyo wanga adzakhala odzaza ndi chisoni kufikira liti?Kodi mdani wanga adzadzikweza pamaso panga kufikira liti?+   Ndiyang’aneni. Ndiyankheni, inu Yehova Mulungu wanga.Walitsani maso anga+ kuti ndisagone mu imfa.+   Chitani zimenezi kuti mdani wanga asanene kuti: “Ndamugonjetsa!”Kutinso adani anga asakondwere chifukwa chakuti ine ndadzandira.+   Koma ine ndakhulupirira kukoma mtima kwanu kosatha.+Mtima wanga ukondwere chifukwa cha chipulumutso chanu.+   Ndidzaimbira Yehova chifukwa wandifupa ndi zinthu zabwino.+

Mawu a M'munsi