Salimo 135:1-21
135 Tamandani Ya, anthu inu!+Tamandani dzina la Yehova,+Mutamandeni, inu atumiki a Yehova,+
2 Inu amene mukuimirira m’nyumba ya Yehova,+M’mabwalo a nyumba ya Mulungu wathu.+
3 Tamandani Ya, pakuti Yehova ndi wabwino.+Muimbireni nyimbo zotamanda dzina lake, pakuti kuchita zimenezi n’kosangalatsa.+
4 Ya wadzisankhira Yakobo,+Wadzisankhira Isiraeli kukhala chuma chake chapadera.+
5 Ine ndikudziwa bwino kuti Yehova ndi wamkulu,+Ndipo Ambuye wathu ndi woposa milungu ina yonse.+
6 Chilichonse chimene Yehova anafuna kuchita anachita.+Anachita zimenezi kumwamba, padziko lapansi, m’nyanja ndi m’madzi onse akuya.+
7 Amachititsa nthunzi kukwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+Iye anapanganso zipata zotulukirapo mvula.+Amachititsa mphepo kutuluka m’nkhokwe zake.+
8 Wochita zimenezi ndiye anapha ana oyamba kubadwa a ku Iguputo,+Anapha ana a anthu ngakhalenso ana a nyama.+
9 Anasonyeza zizindikiro ndi kuchita zozizwitsa pakati pako Iguputo iwe,+Anachita zimenezo kwa Farao ndi kwa atumiki ake onse.+
10 Amene anachita zimenezi ndi amene anakantha mitundu yambiri+Ndi kupha mafumu amphamvu.+
11 Anaphanso Sihoni mfumu ya Aamori+Ndi Ogi mfumu ya Basana,+Ndipo anafafaniza maufumu onse a ku Kanani.+
12 Dziko lawo analipereka kukhala cholowa,+Cholowa cha anthu ake Aisiraeli.+
13 Inu Yehova, dzina lanu lidzakhalapo mpaka kalekale.+Inu Yehova, dzina lanu* lidzakhalapo ku mibadwomibadwo.+
14 Pakuti Yehova adzaweruzira anthu ake mlandu,+Ndipo adzamvera chisoni atumiki ake.+
15 Mafano a anthu a mitundu ina ndi opangidwa ndi siliva ndi golide,+Ntchito ya manja a munthu wochokera kufumbi.+
16 Pakamwa ali napo koma salankhula.+Maso ali nawo koma saona.+
17 Makutu ali nawo koma satha kumva.+Komanso m’mphuno mwawo mulibe mpweya.+
18 Amene amawapanga adzafanana nawo,+Onse amene amawakhulupirira adzakhala ngati mafanowo.+
19 Inu nyumba ya Isiraeli, tamandani Yehova.+Inu nyumba ya Aroni, tamandani Yehova.+
20 Inu nyumba ya Levi, tamandani Yehova.+Inu oopa Yehova, tamandani Yehova.+
21 Yehova amene akukhala ku Yerusalemu,+Atamandidwe mu Ziyoni.+Tamandani Ya, anthu inu!+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “chikumbutso chanu.”