Salimo 52:1-9
Kwa wotsogolera nyimbo. Masikili.* Salimo la Davide, pa nthawi imene Doegi, Mwedomu, anapita kwa Sauli kukamuuza kuti Davide wapita kunyumba ya Ahimeleki.+
52 N’chifukwa chiyani ukudzitukumula chifukwa cha zinthu zoipa, wamphamvu iwe?+Kukoma mtima kosatha kwa Mulungu n’kokhalitsa.+
2 Lilime lako limakonza chiwembu, ndipo ndi lakuthwa ngati lezala,+Limachita zachinyengo.+
3 Umakonda kwambiri zinthu zoipa kuposa zabwino,+Umakonda kwambiri kulankhula chinyengo kuposa kulankhula chilungamo.+ [Seʹlah.]
4 Umakonda mawu onse owononga,+Lilime lachinyengo iwe.+
5 Mulungu adzakupasula kosatha.+Adzakugwetsa ndi kukukokera kunja kwa hema wako,+Ndipo adzakuzula ndithu m’dziko la anthu amoyo.+ [Seʹlah.]
6 Olungama adzaona zimenezi ndi kuchita mantha,+Ndipo adzamuseka.+
7 Munthu wamphamvu wotere sadalira Mulungu monga malo ake achitetezo,+Koma amadalira kuchuluka kwa chuma chake,+Ndipo chitetezo chake amachipeza m’mavuto amene iyeyo amawachititsa.+
8 Koma ine ndidzakhala ngati mtengo waukulu wa maolivi+ wa masamba obiriwira m’nyumba ya Mulungu.Ndidzakhulupirira kukoma mtima kosatha kwa Mulungu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+
9 Ndidzakutamandani mpaka kalekale, chifukwa cha zimene mwachita.+Ndipo ndidzayembekezera dzina lanu pamaso pa okhulupirika anu, chifukwa ndi labwino.+