Salimo 74:1-23

Masikili.* Salimo la Asafu.+ 74  Inu Mulungu, n’chifukwa chiyani mwatitaya?+N’chifukwa chiyani mkwiyo wanu ukuyakira nkhosa zimene mukuweta?+   Kumbukirani anthu amene munawatenga kukhala anu kalelo,+Fuko limene munaliwombola monga cholowa chanu,+Ndi phiri la Ziyoni ili mmene inu mukukhala.+   Pitani kumalo amene awonongedwa.+M’malo oyera, mdani wachitira zoipa china chilichonse.+   Anthu amene akukuchitirani zoipa afuula mosangalala kuti apambana m’malo anu olambiriramo.+Aikamo mbendera zawo monga zizindikiro.+   Iwo amatchuka ngati munthu amene amagwetsa mitengo ndi nkhwangwa m’nkhalango.   Ndipo tsopano zojambula mochita kugoba za m’makoma a malo opatulika, onse amazichotsa ndi nkhwangwa komanso ndodo zokhala ndi chitsulo kumutu kwake.+   Iwo atentha malo anu opatulika.+Aipitsa ndi kugwetsera pansi chihema chokhala ndi dzina lanu.+   Iwo, ngakhalenso ana awo, onse pamodzi anena mumtima mwawo kuti:“Malo onse olambiriramo a Mulungu ayenera kutenthedwa m’dzikoli.”+   Zizindikiro zathu sitinazione, ndipo palibenso mneneri amene watsala,+Pakati pathu palibe amene akudziwa kuti zikhala choncho mpaka liti. 10  Inu Mulungu, kodi mdani adzakuchitirani mopanda ulemu kufikira liti?+Kodi mdani adzanyoza dzina lanu kwamuyaya?+ 11  N’chifukwa chiyani mwachotsa dzanja lanu, dzanja lanu lamanja,+Pachifuwa panu koma osachitapo kanthu? Kodi mukatero ife sitiwonongedwa? 12  Koma Mulungu ndi Mfumu yanga kuyambira kalekale,+Iye ndiye wondipatsa chipulumutso chachikulu padziko lapansi.+ 13  Inu munavundula nyanja ndi mphamvu zanu.+Pakati pa madzi munadula mitu ya zilombo za m’nyanja.+ 14  Inu munaphwanya mitu ya Leviyatani*+ kukhala zidutswazidutswa.Munaipereka kwa anthu monga chakudya, munaipereka kwa anthu okhala m’madera opanda madzi.+ 15  Ndinu amene munang’amba nthaka ndi kupanga akasupe ndi makwawa.+Inu munaumitsa mitsinje imene inali kukhala ndi madzi nthawi zonse.+ 16  Usana ndi wanu, usikunso ndi wanu.+Inu munapanga chounikira, munapanga dzuwa.+ 17  Ndinu amene munaika malire onse a dziko lapansi.+Munapanga nyengo yachilimwe ndi nyengo yachisanu.+ 18  Kumbukirani izi: Inu Yehova, mdani wakuchitirani mopanda ulemu,+Ndipo anthu opusa anyoza dzina lanu.+ 19  Musapereke moyo wa njiwa yanu kwa chilombo chakuthengo.+Musaiwale kwamuyaya moyo wa anthu anu osautsika.+ 20  Kumbukirani pangano limene munachita nafe,+Pakuti malo a mdima a dziko lapansi adzaza ndi chiwawa.+ 21  Musalole kuti munthu woponderezedwa achite manyazi.+Munthu wosautsika ndi wosauka atamande dzina lanu.+ 22  Nyamukani inu Mulungu, weruzani mlandu wanu.+Kumbukirani mmene munthu wopusa wakunyozerani tsiku lonse.+ 23  Musaiwale mawu a anthu amene akukuchitirani zoipa.+Phokoso la anthu okuukirani likukwera kumwamba nthawi zonse.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Sl 32:Kamutu.
Kapena kuti “ng’ona.”