Salimo 78:1-72
Masikili.* Salimo la Asafu.+
78 Inu anthu anga, mvetserani chilamulo changa.+Tcherani khutu ku mawu a pakamwa panga.+
2 Ndidzatsegula pakamwa panga ndi kunena mwambi.+Ndidzanena mawu ophiphiritsa akalekale,+
3 Amene tinamva ndipo tikuwadziwa,+Komanso amene makolo athu anatifotokozera.+
4 Mbadwa zawo sitikuzibisira mawu ophiphiritsawa,+Ndipo tidzawasimba ngakhale ku mibadwo ya m’tsogolo.+Tidzasimba ntchito zotamandika za Yehova ndi mphamvu zake,+Komanso zinthu zodabwitsa zimene wachita.+
5 Mulungu anaika chikumbutso pakati pa ana a Yakobo,+Iye anaika chilamulo mu Isiraeli,+Zinthu zimene analamula makolo athu,+Kuti auze ana awo.+
6 Kuti m’badwo wa m’tsogolo, ana amene adzabadwe m’tsogolo, adzadziwe zimenezi,+Kuti nawonso adzanyamuke ndi kusimbira ana awo.+
7 Kuti anawo azidzadalira Mulungu,+Ndi kuti asadzaiwale zochita za Mulungu+ koma kuti azidzasunga malamulo ake.+
8 Ndipo asadzakhale ngati makolo awo,+M’badwo wosamva ndi wopanduka,+M’badwo umene sunakonze mtima wawo,+Ndipo maganizo awo sanali okhulupirika kwa Mulungu.+
9 Ana a Efuraimu, ngakhale kuti anali ndi mivi ndi mauta,+Anathawa pa tsiku lankhondo.+
10 Iwo sanasunge pangano la Mulungu,+Ndipo anakana kutsatira chilamulo chake.+
11 Iwo anayambanso kuiwala zochita zake,+Ndi ntchito zake zodabwitsa zimene anawaonetsa.+
12 Mulungu anachita zodabwitsa pamaso pa makolo awo+M’dziko la Iguputo,+ m’dera la Zowani.+
13 Iye anagawa nyanja kuti iwo awoloke,+Ndipo anaimitsa madzi kukhala ngati khoma.+
14 Iye anapitiriza kuwatsogolera ndi mtambo masana,+Ndipo usiku wonse anali kuwatsogolera ndi kuwala kwa moto.+
15 Iye anang’amba miyala m’chipululu+Kuti awapatse madzi akumwa ochuluka ngati a m’nyanja.+
16 Iye anatulutsa madzi ambiri pathanthwe,+Ndipo anachititsa madzi kutsika ngati mitsinje.+
17 Koma iwo anapitiriza kumuchimwira+Mwa kupandukira Wam’mwambamwamba m’dera lopanda madzi.+
18 Iwo anapitiriza kuyesa Mulungu m’mitima yawo+Mwa kupempha chakudya china chimene mtima wawo unalakalaka.+
19 Pamenepo anayamba kulankhula mawu oipa kwa Mulungu.+Iwo anati: “Kodi Mulungu angathe kutipatsa chakudya m’chipululu muno?”+
20 Taonani! Kodi Mulungu si uja anamenya thanthwe+Kuti madzi atuluke, kutinso patuluke mitsinje yodzaza madzi?+Koma iwo anati: “Kodi angathenso kutipatsa chakudya,+Kapena kodi angakonzere anthu ake chakudya?”+
21 Choncho Yehova anamva zimenezo ndipo anakwiya.+Moti moto unayakira Yakobo,+Ndipo mkwiyo unatsikira pa Isiraeli.+
22 Pakuti iwo sanakhulupirire Mulungu.+Sanakhulupirire kuti iye adzawapulumutsa.+
23 Pamenepo Mulungu analamula mitambo ya m’mlengalenga,Ndipo anatsegula zitseko zakumwamba.+
24 Ndipo anapitiriza kuwagwetsera mana ngati mvula kuti adye.+Iye anawapatsa tirigu wochokera kumwamba.+
25 Anthu anadya chakudya cha amphamvu.+Iye anawatumizira chakudya chokwanira.+
26 Anachititsa mphepo ya kum’mawa kuwomba m’mlengalenga,+Ndipo mwa mphamvu zake anachititsa mphepo ya kum’mwera kuwomba.+
27 Iye anagwetsa chakudya pa iwo ngati fumbi.+Anawagwetsera zolengedwa zamapiko zouluka, zochuluka ngati mchenga wakunyanja.+
28 Anapitiriza kuwagwetsera zimenezi mumsasa wake,+Kuzungulira mahema ake onse.+
29 Iwo anadya ndi kukhuta kwambiri.+Iye anawabweretsera zimene anali kulakalaka.+
30 Iwo anafunabe chakudya china,Pamene china chinali m’kamwa.+
31 Nthawi yomweyo, mkwiyo wa Mulungu unatsikira pa iwo.+Iye anayamba kupha anthu awo amphamvu.+Ndipo anakomola anyamata a mu Isiraeli.
32 Ngakhale zinali choncho, iwo anawonjezera machimo awo,+Ndipo sanakhulupirire ntchito zake zodabwitsa.+
33 Choncho anathetsa masiku a moyo wawo ngati mpweya wotuluka m’mphuno.+Anadula zaka za moyo wawo ndi masoka.
34 Nthawi zonse akayamba kuwapha, iwo anali kumufunafuna.+Anali kutembenuka ndi kuyamba kufunafuna Mulungu.+
35 Iwo anali kukumbukira kuti Mulungu anali Thanthwe lawo,+Ndiponso kuti Mulungu Wam’mwambamwamba anali Wowabwezerera.+
36 Koma iwo anali kufuna kum’pusitsa ndi pakamwa pawo.+Ndi lilime lawo anali kufuna kunena bodza kwa iye.+
37 Mtima wawo sunali wokhulupirika kwa iye.+Ndipo iwo sanakhulupirike ku pangano lake.+
38 Koma anawamvera chifundo.+ Anali kukhululukira* machimo awo+ ndipo sanali kuwawononga.+Nthawi zambiri anali kubweza mkwiyo wake,+Ndipo sanali kuwasonyeza ukali wake wonse.
39 Iye anali kukumbukira nthawi zonse kuti iwo ndi anthu athupi la nyama,+Anali kukumbukira kuti moyo wawo umachoka ndipo subwereranso.+
40 Iwo analitu kumupandukira kawirikawiri m’chipululu,+Anali kumukhumudwitsa m’chipululumo!+
41 Mobwerezabwereza, anali kumuyesa Mulungu,+Ndipo anali kumvetsa chisoni Woyera wa Isiraeli.+
42 Iwo sanakumbukire dzanja la Mulungu,+Sanakumbukire tsiku limene anawawombola kwa mdani wawo,+
43 Iwo sanakumbukire mmene anaikira zizindikiro zake mu Iguputo,+Ndi zozizwitsa zimene anachita m’dera la Zowani,+
44 Mmene anasinthira mitsinje ing’onoing’ono yotuluka mumtsinje wa Nailo kukhala magazi,+Moti sanathe kumwa madzi ake.+
45 Mulungu anawatumizira tizilombo toyamwa magazi kuti tiwadye,+Ndi achule kuti awawononge.+
46 Anapereka zokolola zawo kwa mphemvu,Ndipo ntchito yawo yolemetsa anaipereka kwa dzombe.+
47 Anapha mitengo yawo ya mpesa ndi mvula yamatalala.+Anapha mitengo yawo ya mkuyu ndi matalala.+
48 Anaphanso nyama zawo zonyamula katundu ndi matalala,+Ndiponso ziweto zawo ndi mliri wakupha.
49 Anawasonyeza mkwiyo wake woyaka moto,+Ukali, ziweruzo zamphamvu ndi masautso.+Anawatumizira makamu a angelo obweretsa masoka.+
50 Mkwiyo wake anaulambulira njira.+Sanawabweze kuwachotsa ku imfa.Ndipo anawapha ndi mliri.+
51 Pamapeto pake anapha ana onse oyamba kubadwa mu Iguputo,+Amene ndi chiyambi cha mphamvu zawo zobereka m’mahema a Hamu.+
52 Kenako anachititsa anthu ake kuchoka m’dzikolo ngati gulu la nkhosa,+Anawayendetsa m’chipululu ngati gulu la ziweto.+
53 Anapitiriza kuwatsogolera ndi kuwateteza ndipo iwo sanachite mantha.+Nyanja inamiza adani awo.+
54 Kenako anawalowetsa m’dziko lake lopatulika,+M’dera lamapiri ili limene dzanja lake lamanja linatenga.+
55 Chifukwa cha iwo anachotsa mitundu ina pang’onopang’ono m’dzikoli,+Ndipo anayesa dzikoli ndi kuligawa kwa iwo kukhala cholowa chawo,+Moti anachititsa mafuko a Isiraeli kukhala m’nyumba zawozawo.+
56 Koma iwo anayamba kuyesa Mulungu Wam’mwambamwamba ndi kum’pandukira,+Ndipo sanasunge zikumbutso zake.+
57 Iwo anali kubwerera ndi kuchita zinthu mwachinyengo ngati makolo awo.+Anapotoka maganizo ngati uta wosakunga kwambiri.+
58 Iwo anapitiriza kumukhumudwitsa ndi malo awo okwezeka,+Ndipo anamuchititsa nsanje ndi zifaniziro zawo zogoba.+
59 Mulungu anamva+ ndipo anakwiya kwambiri.+Chotero ananyansidwa kwambiri ndi Isiraeli.+
60 Pamapeto pake anasiya chihema chopatulika cha ku Silo,+Hema limene anali kukhalamo pakati pa anthu ochokera kufumbi.+
61 Analola kuti chizindikiro cha mphamvu zake chitengedwe ndi adani ake,+Iye analola kuti chizindikiro cha kukongola kwake chikhale m’manja mwa adani.+
62 Iye anapereka anthu ake ku lupanga,+Ndipo anakwiyira cholowa chake.+
63 Anyamata ake ananyeka ndi moto,Ndipo anamwali ake sanatamandidwe.+
64 Ansembe ake anagwa ndi lupanga,+Ndipo akazi awo amasiye sanalire.+
65 Pamenepo Yehova anagalamuka ngati akudzuka kutulo,+Ngati munthu wamphamvu amene akugalamuka pambuyo pomwa vinyo wambiri.+
66 Iye anathamangitsa adani ake ndi kuwapha.+Anawachititsa kuti akhale akutonzedwa mpaka kalekale.+
67 Iye anakana hema wa Yosefe,+Ndipo sanasankhe fuko la Efuraimu.+
68 Koma anasankha fuko la Yuda,+Phiri la Ziyoni limene analikonda.+
69 Anayamba kumanga malo opatulika ngati malo okwera a paphiri,+Ngati dziko lapansi limene analikhazikitsa mpaka kalekale.+
70 Choncho anasankha Davide mtumiki wake,+Ndipo anamuchotsa kumakola a nkhosa.+
71 Anamutenga kumene anali kuweta nkhosa zoyamwitsa,+Anamutenga kuti akhale m’busa wa ana a Yakobo amene ndi anthu ake,+Ndi Isiraeli, amene ndi cholowa chake.+
72 Iye anayamba kuwaweta malinga ndi mtima wake wosagawanika,+Ndipo anayamba kuwatsogolera mwaluso.+