Salimo 44:1-26
Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la ana a Kora.+ Masikili.*
44 Inu Mulungu, ife tamva ndi makutu athu,Makolo athu anatifotokozera+Ntchito zimene inu munachita m’masiku awo,+M’masiku akale.+
2 Munapitikitsa anthu a mitundu ina ndi dzanja lanu,+Ndipo m’malo mwawo munakhazikitsa anthu anu.+Munagonjetsa mitundu ya anthu ndi kuipitikitsa.+
3 Pakuti iwo sanatenge dzikolo chifukwa cha lupanga lawo,+Ndipo si mkono wawo umene unawabweretsera chipulumutso.+Koma chinabwera ndi dzanja lanu lamanja,+ mkono wanu ndi kuwala kwa nkhope yanu,Chifukwa munakondwera nawo.+
4 Inu Mulungu, ndinu Mfumu yanga.+Lamulani kuti Yakobo alandire chipulumutso chachikulu.+
5 Ndi thandizo lanu tidzakankha adani athu.+M’dzina lanu tidzapondereza amene akutiukira.+
6 Pakuti sindinadalire uta wanga,+Ndipo si lupanga langa limene linandipulumutsa.+
7 Ndinu amene munatipulumutsa kwa adani athu,+Ndipo munanyazitsa anthu amene amadana nafe kwambiri.+
8 Tidzayamika Mulungu nthawi zonse,+Tidzatamanda dzina lanu mpaka kalekale.+ [Seʹlah.]
9 Koma tsopano mwatitaya ndi kutichititsa manyazi,+Simukuyenda ndi magulu athu ankhondo.+
10 Mwachititsa kuti tithawe pamaso pa adani athu,+Ndipo anthu odana nafe kwambiri afunkha zinthu zathu.+
11 Mwatipereka kwa adani athu kuti atidye ngati nkhosa,+Ndipo mwatimwaza pakati pa anthu a mitundu ina.+
12 Mwagulitsa anthu anu pa mtengo wotsika kwambiri,+Ndipo simunapeze phindu ndi mtengo wawo.
13 Mwatisandutsa chitonzo kwa anthu oyandikana nafe,+Mwatisandutsa chinthu chonyozeka ndi choseketsa kwa onse otizungulira.+
14 Mwatisandutsa mwambi pakati pa anthu a mitundu ina,+Mwatisandutsa anthu amene anthu a mitundu inawo akuwapukusira mitu.+
15 Zondichititsa manyazi zili pamaso panga tsiku lonse,Ndipo manyazi aphimba nkhope yanga,+
16 Chifukwa cha mawu a munthu wonditonza ndi wolankhula zachipongwe,Ndiponso chifukwa cha mdani wanga ndi wofuna kundibwezera choipa.+
17 Zonsezi ndi zimene zatigwera, koma sitinakuiwaleni,+Sitinachite mwachinyengo ndi pangano lanu.+
18 Mitima yathu sinakhale yosakhulupirika n’kuchoka panjira yanu,+Ndipo mapazi athu sanapatuke panjira yanu.+
19 Pakuti inu mwatiphwanya kumalo amene mimbulu imasonkhana,+Mwatiphimba ndi mdima wandiweyani.+
20 Ngati tikanaiwala dzina la Mulungu wathu,Kapena kupemphera kwa mulungu wachilendo titakweza manja athu,+
21 Kodi Mulungu sakanafufuza zimenezi?+Pakuti iye amadziwa zinsinsi za mumtima.+
22 Koma chifukwa cha inu, tikuphedwa nthawi zonse.Takhala ngati nkhosa zokaphedwa.+
23 Nyamukani. N’chifukwa chiyani mukugonabe, inu Yehova?+Dzukani. Musatitaye kwamuyaya.+
24 N’chifukwa chiyani mukubisabe nkhope yanu?N’chifukwa chiyani mukuiwala masautso athu ndi kuponderezedwa kwathu?+
25 Pakuti miyoyo yathu yasautsika.+Mimba zathu zili thasa! padothi.
26 Nyamukani kuti mutithandize+Tiwomboleni chifukwa cha kukoma mtima kwanu kosatha.+