Salimo 65:1-13

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la Davide. 65  Inu Mulungu, anthu akukutamandani mu Ziyoni+ ndipo akhala chete pamaso panu,Iwo adzakwaniritsa malonjezo awo kwa inu.+   Inu Wakumva pemphero, anthu a mitundu yonse adzabwera kwa inu.+   Zolakwa zanga zandikulira.+Inu mudzatikhululukira* machimo athu.+   Wodala ndi munthu amene inu mwamusankha ndi kumuyandikizitsa kwa inu,+Kuti akhale m’mabwalo anu.+Tidzakhutira ndi zinthu zabwino za m’nyumba yanu,+Malo anu oyera kapena kuti kachisi wanu woyera.+   Mudzatiyankha ndi zinthu zochititsa mantha zochitika mwachilungamo,+Inu Mulungu wa chipulumutso chathu,+Inu Chidaliro cha malire onse a dziko lapansi ndi anthu okhala pafupi ndi nyanja zakutali.+   Ndi mphamvu zake, iye akukhazikitsa mapiri,+Iye wamanga mphamvu zochuluka m’chiuno mwake.+   Iye akutontholetsa phokoso la nyanja,+Akutontholetsa phokoso la mafunde ake komanso chipwirikiti cha mitundu ya anthu.+   Ndipo anthu okhala m’madera akutali adzachita mantha ndi zizindikiro zanu,+Mudzachititsa kulowa ndi kutuluka kwa dzuwa kufuula mokondwera.+   Inu mwatembenukira dziko lapansi kuti mulipatse zinthu zochuluka,+Mwalilemeretsa kwambiri.Mtsinje wochokera kwa Mulungu ndi wosefukira ndi madzi.+Munalinganiza zinthu, kuti mbewu zawo zibale.+Umu ndi mmene mumaperekera zinthu padziko lapansi.+ 10  Mizere yawo imakhathamira, ndipo zibuma zake zimasalazidwa,+Ndipo mumafewetsa nthaka ndi mvula yamvumbi. Mumadalitsa zomera m’nthakayo.+ 11  Mwaveka chaka chisoti chachifumu cha ubwino wanu,+Ndipo njira zanu zikukha mafuta.+ 12  Malo odyetserako ziweto a m’chipululu akukha mafuta,+Ndipo zitunda zamangirira chisangalalo m’chiuno mwawo.+ 13  Malo odyetserako ziweto adzaza ndi nkhosa,+Ndipo zigwa zakutidwa ndi tirigu.+Malo onsewa akufuula mosangalala ndi kuimba chifukwa cha kupambana.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “mudzaphimba.”