Salimo 71:1-24
71 Inu Yehova, ine ndathawira kwa inu.+Musalole kuti ndichite manyazi.+
2 Mundilanditse chifukwa cha chilungamo chanu ndipo mundipulumutse.+Tcherani khutu lanu kwa ine ndi kundipulumutsa.+
3 Mukhale thanthwe lachitetezo loti ndizilowamo nthawi zonse.+Lamulani kuti ndipulumutsidwe,+Pakuti inu ndinu thanthwe langa ndi malo anga achitetezo.+
4 Inu Mulungu wanga, ndipulumutseni m’manja mwa woipa,+Ndipulumutseni m’manja mwa munthu wochita zinthu mopanda chilungamo komanso mopondereza.+
5 Pakuti chiyembekezo changa ndinu,+ Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, ndimadalira inu kuyambira pa unyamata wanga.+
6 Kuyambira ndili m’mimba mwa mayi anga inu mwandithandiza.+Inu ndi amene munanditulutsa m’mimba mwa mayi anga.+Ndimatamanda inu nthawi zonse.+
7 Ndakhala ngati chozizwitsa kwa anthu ambiri,+Koma inu ndinu malo anga olimba othawirako.+
8 M’kamwa mwanga mwadzaza mawu otamanda inu,+Ndipo pakamwa panga pakunena za ulemerero wanu tsiku lonse.+
9 Musanditaye nthawi ya ukalamba wanga.+Musandisiye pa nthawi imene mphamvu zanga zikutha.+
10 Pakuti adani anga anena za ine,+Ndipo anthu olondalonda moyo wanga, onse pamodzi achita upo,+
11 Iwo akunena kuti: “Mulungu wamusiya.+Mulondoleni ndi kumugwira pakuti palibe womulanditsa.”+
12 Inu Mulungu, musakhale kutali ndi ine.+Inu Mulungu wanga, fulumirani kundithandiza.+
13 Anthu otsutsana nane achite manyazi, iwo awonongedwe.+Amene akufunafuna kundigwetsera tsoka adziphimbe ndi chitonzo ndiponso manyazi.+
14 Koma ine ndidzayembekezera inu nthawi zonse,+Ndipo ndidzakutamandani mowirikiza kuposa kale.
15 Pakamwa panga padzanena za chilungamo chanu,+Padzanena za chipulumutso chanu tsiku lonse,+Pakuti ntchito za chilungamo ndi chipulumutso chanu ndi zochuluka ndipo sindinathe kuziwerenga.+
16 Ndidzabwera ndi kunena za mphamvu zanu zazikulu,+ inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa.+Ndidzanena za chilungamo chanu, osati cha wina aliyense.+
17 Inu Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira pa unyamata wanga,+Ndipo mpaka pano ndikunena za ntchito zanu zodabwitsa.+
18 Ngakhale nditakalamba ndi kumera imvi, inu Mulungu musandisiye,+Kufikira nditanena za dzanja lanu lamphamvu ku m’badwo wotsatira,+Kufikira nditanena za mphamvu zanu kwa onse obwera m’tsogolo.+
19 Chilungamo chanu, inu Mulungu chafika kumwamba.+Tikanena za zinthu zazikulu zimene munachita,+Inu Mulungu, ndani angafanane ndi inu?+
20 Chifukwa chakuti mwandionetsa masautso ndi masoka ambiri,+Nditsitsimutseni.+Nditulutseninso m’madzi akuya, pansi pa nthaka.+
21 Kulitsani ulemu wanga,+Mundizungulire ndi chitetezo chanu ndi kundilimbikitsa.+
22 Inenso ndidzakutamandani ndi chipangizo cha zingwe,+Ndidzatamanda choonadi chanu, inu Mulungu.+Ndidzaimba nyimbo zokutamandani ndi zeze, Inu Woyera wa Isiraeli.+
23 Ndikafuna kuimba nyimbo zokutamandani, pakamwa panga padzafuula mokondwera,+Ngakhalenso moyo wanga umene mwauwombola+ udzakutamandani.
24 Ngakhalenso lilime langa lidzalankhula chapansipansi za chilungamo chanu tsiku lonse,+Pakuti ofunafuna kundigwetsera tsoka achita manyazi ndipo athedwa nzeru.+