Salimo 20:1-9

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide. 20  Yehova akuyankheni pa tsiku la nsautso.+Dzina la Mulungu wa Yakobo likutetezeni.+   Atumize thandizo kuchokera kumalo oyera.+Akuchirikizeni ali ku Ziyoni.+   Akumbukire nsembe zanu zonse zimene munapereka monga mphatso.+Alandire mafuta a nsembe zanu zopsereza.+ [Seʹlah.]   Akupatseni zokhumba za mtima wanu,+Ndipo akwaniritse zofuna zanu.+   Tidzafuula mokondwera chifukwa cha chipulumutso chanu,+Tidzakweza mbendera zathu m’dzina la Mulungu wathu.+Yehova akwaniritse zopempha zanu zonse.+   Tsopano ndadziwa kuti Yehova amapulumutsa wodzozedwa wake.+Amamuyankha kuchokera kumwamba kwake koyera,+Amamupulumutsa ndi dzanja lake lamanja lamphamvu zopulumutsa.+   Ena akunena za magaleta* ndipo ena akunena za mahatchi,*+Koma ife tidzanena za dzina la Yehova Mulungu wathu.+   Anthu amenewo athyoka ndipo agwa,+Koma ife tanyamuka ndipo taima chilili.+   Inu Yehova, pulumutsani mfumu!+Tsiku limene tidzaitana, Mulungu adzatiyankha.+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Ena amati “mahosi” kapena “akavalo.”