Salimo 122:1-9
Nyimbo ya Davide Yokwerera Kumzinda.
122 Ndinakondwera pamene anandiuza kuti:+“Tiyeni tipite+ kunyumba ya Yehova.”+
2 Mapazi athu anaima+Pazipata zako iwe Yerusalemu.+
3 Mzinda wa Yerusalemu unamangidwa+Ngati chinthu chimodzi chogwirizana,+
4 Mafuko amapita kumeneko,+Mafuko a Ya,+Amapita kumeneko kukatamanda dzina la Yehova+Mogwirizana ndi lamulo loperekedwa kwa Isiraeli.+
5 Kumeneko n’kumene kumakhala mipando yachiweruzo,+Mipando yachifumu ya nyumba ya Davide.+
6 Pemphererani mtendere wa Yerusalemu, anthu inu.+Amene amakukonda, mzinda iwe, sadzakhala ndi nkhawa iliyonse.+
7 M’malo ako otchingidwa ndi khoma lolimba mupitirizebe kukhala mtendere,+Anthu okhala munsanja zako apitirizebe kukhala opanda nkhawa iliyonse.+
8 Tsopano ndikulankhula m’malo mwa abale anga ndi anzanga kuti:+“Mtendere ukhale nawe.”+
9 Chifukwa cha nyumba ya Yehova Mulungu wathu,+Ndidzapitiriza kukupempherera kuti zinthu zikuyendere bwino.+