Salimo 23:1-6
Nyimbo ya Davide.
23 Yehova ndi M’busa wanga.+Sindidzasowa kanthu.+
2 Amandigoneka m’mabusa a msipu wambiri.+Amandiyendetsa m’malo opumira a madzi ambiri.+
3 Amatsitsimula moyo wanga.+Amanditsogolera m’tinjira tachilungamo chifukwa cha dzina lake.+
4 Ngakhale ndikuyenda m’chigwa cha mdima wandiweyani,+Sindikuopa kanthu,+Pakuti inu muli ndi ine.+Chibonga chanu ndi ndodo yanu ndi zimene zimandilimbikitsa.+
5 Mumandipatsa chakudya patebulo, pamaso pa anthu ondichitira zoipa.+Mwadzoza mutu wanga ndi mafuta.+Chikho changa ndi chodzaza bwino.+
6 Ndithudi, ubwino ndi kukoma mtima kosatha zidzanditsata masiku onse a moyo wanga.+Ndipo ine ndidzakhala m’nyumba ya Yehova mpaka kalekale.+