Salimo 103:1-22
Salimo la Davide.
103 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.+Chilichonse mkati mwanga, chitamande dzina lake loyera.+
2 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga,Ndipo usaiwale zochita zake zonse.+
3 Tamanda amene akukukhululukira zolakwa zako zonse,+Iye amene akukuchiritsa matenda ako onse.+
4 Tamanda amene akuwombola moyo wako kudzenje,+Amene akukuveka kukoma mtima kosatha ndi chifundo ngati chisoti chachifumu,+
5 Amene akukukhutiritsa pa nthawi ya moyo wako ndi zinthu zabwino.+Mulungu akukuchititsa kukhalabe wachinyamata ndi wamphamvu ngati chiwombankhanga.+
6 Yehova akuchitira chilungamo+Ndi kuperekera zigamulo anthu amene akuchitiridwa zachinyengo.+
7 Anauza Mose njira zake,+Ndipo anadziwitsa ana a Isiraeli zochita zake.+
8 Yehova ndi wachifundo ndi wachisomo,+Wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha.+
9 Iye sadzakhalira kutiimba mlandu nthawi zonse chifukwa cha zolakwa zathu,+Kapena kutisungira mkwiyo mpaka kalekale.+
10 Sanatichitire mogwirizana ndi machimo athu,+Kapena kutipatsa chilango chogwirizana ndi zolakwa zathu.+
11 Pakuti monga mmene kumwamba kulili pamwamba kwambiri kuposa dziko lapansi,+Kukoma mtima kwake kosatha nakonso ndi kwapamwamba kwa onse omuopa.+
12 Monga mmene kum’mawa kwatalikirana ndi kumadzulo,+Momwemonso, watiikira kutali zolakwa zathu.+
13 Monga mmene bambo amasonyezera chifundo kwa ana ake,+Yehova wasonyezanso chifundo kwa onse omuopa.+
14 Pakuti iye akudziwa bwino mmene anatiumbira,+Amakumbukira kuti ndife fumbi.+
15 Masiku a moyo wa munthu ali ngati masiku a udzu wobiriwira.+Iye amaphuka ngati mmene duwa lakutchire limaphukira.+
16 Mphepo ikawomba limafa,+Ndipo pamalo amene linali sipadziwikanso,+
17 Koma Yehova adzapitiriza kusonyeza kukoma mtima kwake kosatha mpaka kalekale,+Kwa anthu amene amamuopa.+Ndipo adzapitiriza kusonyeza chilungamo chake kwa ana a ana awo.+
18 Adzapitiriza kuchita zimenezi kwa anthu osunga pangano lake,+Ndi kwa anthu okumbukira malamulo ake ndi kuwatsatira.+
19 Yehova wakhazikitsa mpando wake wachifumu kumwamba.+Ndipo ufumu wake ukulamulira chilichonse.+
20 Tamandani Yehova, inu angelo+ ake amphamvu, ochita zimene wanena,+Mwa kumvera malamulo ake.+
21 Tamandani Yehova inu makamu ake onse,+Inu atumiki ake onse ochita chifuniro chake.+
22 Tamandani Yehova inu ntchito zake zonse,+M’malo onse amene iye akulamulira.+Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.+