Salimo 50:1-23
Nyimbo ya Asafu.+
50 Wamphamvuyo,+ Yehova, Mulungu,+ walankhula+Ndipo akuitana dziko lapansi,+Kuchokera kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera.+
2 Mulungu wawala ali ku Ziyoni,+ mzinda wokongola kwambiri.+
3 Mulungu wathu adzabwera ndipo sadzakhala chete.+Pamaso pake pali moto wonyeketsa,+Ndipo pamalo onse omuzungulira pali mkuntho wamphamvu.+
4 Akuitana kumwamba ndi dziko lapansi+Kuti apereke chiweruzo kwa anthu ake. Iye akuti:+
5 “Sonkhanitsani okhulupirika anga kwa ine,+Amene achita pangano mwa kupereka nsembe.”+
6 Ndipo kumwamba kukunena za chilungamo chake,+Pakuti Mulungu ndiye Woweruza.+ [Seʹlah.]
7 “Ndimvereni anthu anga, ndipo ine ndilankhula,+Inu Aisiraeli, ine ndipereka umboni wotsutsana nanu.+Ine ndine Mulungu, Mulungu wanu.+
8 Sindikukudzudzulani chifukwa cha nsembe zanu,+Kapena chifukwa cha nsembe zanu zopsereza zathunthu zimene mumapereka kwa ine nthawi zonse.+
9 Sindidzatenga ng’ombe yamphongo m’nyumba yanu,+Kapena mbuzi yamphongo m’makola anu.
10 Pakuti nyama iliyonse yakutchire ndi yanga,+Ndiponso nyama zopezeka m’mapiri 1,000.+
11 Ndikudziwa bwino zolengedwa zonse zouluka za m’mapiri,+Ndipo magulu a nyama zakutchire ndi anga.+
12 Ngakhale nditakhala ndi njala, sindingakuuze,Pakuti dziko lonse+ ndiponso zonse za mmenemo ndi zanga.+
13 Kodi ndiyenera kudya nyama ya ng’ombe zamphongo zonenepa,+Kapena kumwa magazi a mbuzi zamphongo?+
14 Pereka nsembe zoyamikira kwa Mulungu,+Ndipo pereka kwa Wam’mwambamwamba zimene walonjeza.+
15 Pa tsiku la nsautso undiitane.+Ine ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.”+
16 Koma Mulungu adzauza woipa kuti:+“Ndani wakupatsa udindo wofotokoza malangizo anga,+Ndi wolankhula za pangano langa?+
17 Iwe umadana ndi malangizo,*+Ndipo umaponya mawu anga kunkhongo.+
18 Nthawi zonse ukaona wakuba unali kusangalala naye.+Ndipo unali kugwirizana ndi anthu achigololo.+
19 Walekerera pakamwa pako kulankhula zinthu zoipa,+Ndipo ukugwiritsa ntchito lilime lako kulankhula zachinyengo.+
20 Umakhala pansi ndi kunenera m’bale wako zinthu zoipa,+Umapezera zifukwa mwana wamwamuna wa mayi ako.+
21 Wachita zinthu zonsezi, koma ine ndinakhala chete.+Unali kuganiza kuti ine ndikhala ngati iwe.+Ine ndidzakudzudzula,+ ndipo ndidzaika machimo ako onse poyera iwe ukuona.+
22 Zindikirani zimenezi, anthu oiwala Mulungu inu,+Kuti ndisakukhadzulekhadzuleni popanda aliyense wokupulumutsani.+
23 Amene akupereka nsembe yoyamikira kwa ine ndi amene akundilemekeza.+Ndipo amene akuyenda panjirayo motsimikiza,Ndidzamuonetsa chipulumutso changa.”+