Salimo 86:1-17
Pemphero la Davide.
86 Tcherani khutu inu Yehova. Ndiyankheni,+Pakuti ndasautsika ndipo ndasauka.+
2 Tetezani moyo wanga pakuti ndine wokhulupirika.+Inu ndinu Mulungu wanga, pulumutsani mtumiki wanu amene amakukhulupirirani.+
3 Ndikomereni mtima inu Yehova,+Pakuti ndimaitana inu tsiku lonse.+
4 Sangalatsani mtima wa ine mtumiki wanu,+Pakuti ndapereka moyo wanga kwa inu Yehova.+
5 Pakuti inu Yehova ndinu Mulungu wabwino+ ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka.+Kukoma mtima kosatha kumene mumawasonyeza onse oitana pa inu ndi kwakukulu.+
6 Inu Yehova, tcherani khutu ku pemphero langa.+Ndipo mvetserani mawu a kuchonderera kwanga.+
7 Pa tsiku la nsautso yanga ndidzaitana pa inu,+Ndipo inu mudzandiyankha.+
8 Inu Yehova, palibe mulungu wina amene angafanane ndi inu.+Ndipo palibe ntchito zilizonse zofanana ndi ntchito zanu.+
9 Mitundu yonse imene munapanga idzabwera kwa inu,+Ndipo idzagwada pamaso panu, inu Yehova,+Ndi kulemekeza dzina lanu.+
10 Pakuti inu ndinu wamkulu ndipo mukuchita zinthu zodabwitsa.+Inu nokha ndinu Mulungu.+
11 Inu Yehova, ndilangizeni za njira yanu.+Ndidzayenda m’choonadi chanu.+Ndipatseni mtima wosagawanika kuti ndiope dzina lanu.+
12 Ndikukutamandani inu Yehova Mulungu wanga ndi mtima wanga wonse,+Ndipo ndidzalemekeza dzina lanu mpaka kalekale,
13 Pakuti kukoma mtima kosatha kumene mwandisonyeza ndi kwakukulu,+Ndipo mwapulumutsa moyo wanga ku Manda, kumalo apansi penipeni.+
14 Inu Mulungu, anthu odzitukumula andiukira.+Khamu la anthu opondereza anzawo likufunafuna moyo wanga,+Ndipo sanakuikeni patsogolo pawo.+
15 Koma inu Yehova, ndinu Mulungu wachifundo ndi wachisomo,+Wosakwiya msanga+ ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi choonadi.+
16 Ndicheukireni ndi kundikomera mtima.+Patsani mtumiki wanu mphamvu,+Ndipo pulumutsani mwana wa kapolo wanu wamkazi.+
17 Ikani chizindikiro cha ubwino wanu pa ine,Kuti anthu odana nane aone zimenezi ndi kuchita manyazi,+Pakuti inu Yehova mwandithandiza ndi kundilimbikitsa.+