Salimo 72:1-20

Salimo lonena za Solomo. 72  Inu Mulungu, dziwitsani mfumu za zigamulo zanu,+Ndipo dziwitsani mwana wa mfumu za chilungamo chanu.+   Aweruzire anthu milandu mwachilungamo,+Ndipo aweruze milandu ya osautsika ndi ziweruzo zolungama.+   Mapiri atenge mtendere ndi kupita nawo kwa anthu,+Komanso zitunda zitenge mtendere wopezeka mwachilungamo.   Aweruze osautsika pakati pa anthu,+Apulumutse ana a anthu osauka,Ndipo aphwanye wobera anzake mwachinyengo.   Iwo adzakuopani nthawi zonse pamene dzuwa likuwala,+Adzakuopani ku mibadwomibadwo pamene mwezi uli kuthambo.+   Adzatsika ngati mvula pa udzu umene wadulidwa,+Ngati mvula yambiri yamvumbi imene imanyowetsa kwambiri nthaka.+   M’masiku ake, wolungama adzaphuka,+Ndipo padzakhala mtendere wochuluka kwa nthawi yonse pamene mwezi udzakhalepo.+   Ndipo adzakhala ndi anthu omugonjera kuchokera kunyanja kukafika kunyanja,+Komanso kuchokera ku Mtsinje*+ kukafika kumalekezero a dziko lapansi.+   Anthu okhala m’madera opanda madzi adzagwada pamaso pake,+Ndipo adani ake adzabwira fumbi.+ 10  Mafumu a ku Tarisi ndi m’zilumba+Adzapereka msonkho.+Mafumu a ku Sheba ndi SebaAdzapereka mphatso.+ 11  Mafumu onse adzamugwadira ndi kumuweramira.+Ndipo mitundu yonse ya anthu idzamutumikira.+ 12  Pakuti adzalanditsa wosauka amene akufuula popempha thandizo,+Komanso wosautsika ndi aliyense wopanda womuthandiza.+ 13  Adzamvera chisoni munthu wonyozeka ndi wosauka,+Ndipo adzapulumutsa miyoyo ya anthu osauka.+ 14  Adzawombola miyoyo yawo ku chipsinjo ndi chiwawa,Ndipo adzaona magazi awo kukhala amtengo wapatali.+ 15  Iye akhale ndi moyo wautali,+ ndipo apatsidwe wina mwa golide wa ku Sheba.+Nthawi zonse anthu azimupempherera.Adalitsike tsiku lililonse.+ 16  Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri.+Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.+Zokolola za mfumu zidzachuluka ngati mitengo ya ku Lebanoni,+Ndipo anthu ochokera mumzinda adzaphuka ngati udzu wa panthaka.+ 17  Dzina lake likhalebe mpaka kalekale.+Nthawi zonse pamene dzuwa latuluka, dzina lake lizitchuka,Ndipo kudzera mwa iye, anthu apeze madalitso.*+Mitundu yonse ya anthu imutche wodala.+ 18  Adalitsike Yehova Mulungu, Mulungu wa Isiraeli,+Iye yekha amene akuchita ntchito zodabwitsa.+ 19  Lidalitsike dzina lake laulemerero mpaka kalekale,+Ndipo ulemerero wake udzaze dziko lonse lapansi.+Ame! Ame!* 20  Mapemphero a Davide mwana wa Jese,+ athera pamenepa.

Mawu a M'munsi

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Kapena kuti “adzadzidalitsa okha,” kusonyeza kuti akufunika kuchitapo kanthu kuti alandire madalitso amenewo.
Kapena kuti “Zikhale momwemo! Zikhale momwemo!”