Salimo 30:1-12
Nyimbo ndi Salimo la Davide lotsegulira nyumba.+
30 Ndidzakutamandani inu Yehova, pakuti mwandipulumutsa,+Ndipo simunalole kuti adani anga akondwere ndi kusautsika kwanga.+
2 Inu Yehova Mulungu wanga, ndinafuulira kwa inu kuti mundithandize ndipo munandichiritsa.+
3 Inu Yehova, mwanditulutsa m’Manda,+Mwandisunga ndi moyo, kuti ndisatsikire m’dzenje.+
4 Imbani nyimbo zotamanda Yehova, inu okhulupirika ake,+Yamikani dzina lake loyera.*+
5 Chifukwa mkwiyo wa Mulungu sukhalitsa pa munthu,+Koma kukoma mtima kwake ndi kwa moyo wonse.+Usiku kumakhala kulira,+ koma m’mawa kumakhala kufuula ndi chisangalalo.+
6 Mtima wanga utakhazikika ndinati:+“Sindidzagwedezeka.”+
7 Inu Yehova, chifukwa chakuti munandikomera mtima munakhazikitsa mwamphamvu phiri langa.+Pamene munabisa nkhope yanu, ndinasokonezeka.+
8 Ndinaitana inu Yehova,+Ndipo ndinachonderera Yehova kuti andikomere mtima.+
9 Kodi magazi anga angakhale ndi phindu lanji ngati nditatsikira kudzenje la manda?+Kodi fumbi lidzakutamandani?+ Kodi lidzalengeza kuti inu ndinu woona?+
10 Imvani inu Yehova, ndi kundikomera mtima.+Inu Yehova, khalani mthandizi wanga.+
11 Mwasintha kulira kwanga kuti kukhale kuvina.+Mwandivula chiguduli* changa ndipo mwandiveka chisangalalo,+
12 Kuti mtima wanga uimbe nyimbo zokutamandani ndipo usakhale chete.+Inu Yehova Mulungu wanga, ndidzakutamandani mpaka kalekale.+