Salimo 5:1-12
Kwa wotsogolera nyimbo pa Nehiloti.* Nyimbo ya Davide.
5 Mvetserani mawu anga+ inu Yehova,Mumvetse kudandaula kwanga.
2 Imvani kufuula kwanga kopempha thandizo,+Inu Mfumu yanga+ ndi Mulungu wanga, chifukwa ndimapemphera kwa inu.+
3 Inu Yehova, m’mawa mudzamva mawu anga,+M’mawa ndidzalankhula nanu ndipo ndidzadikira yankho.+
4 Pakuti inu sindinu Mulungu wokondwera ndi zoipa,+Palibe munthu woipa amene angakhale ndi inu ngakhale kwa kanthawi kochepa.+
5 Palibe anthu odzitama amene angaime pamaso panu.+Mumadana ndi onse ochita zopweteka ena.+
6 Mudzawononga olankhula bodza.+Munthu wokhetsa magazi+ ndi wachinyengo,+ Yehova amaipidwa naye.
7 Koma ine ndidzalowa m’nyumba yanu+Chifukwa cha kuchuluka kwa kukoma mtima kwanu kosatha.+Ndidzawerama nditayang’ana kumene kuli kachisi wanu wopatulika chifukwa chokuopani.+
8 Inu Yehova, nditsogolereni m’chilungamo chanu+ chifukwa adani anga andizungulira.+Salazani njira yanu kuti ndiyendemo popanda chopunthwitsa.+
9 Pakuti m’kamwa mwawo simutuluka mawu okhulupirika.+Mitima yawo yadzaza ndi zinthu zoipa.+Mmero wawo ndi manda otseguka.+Iwo amalankhula ndi lilime lachinyengo.+
10 Mulungu adzawapeza ndi mlandu.+Adzagwa ndi ziwembu zawo zomwe.+Muwamwaze chifukwa cha kuchuluka kwa zolakwa zawo,+Chifukwa iwo akupandukirani.+
11 Koma onse othawira kwa inu adzakondwa.+Adzafuula mokondwera mpaka kalekale.*+Ndipo inu mudzawateteza.Okonda dzina lanu adzakondwa chifukwa cha inu.+
12 Pakuti inu Yehova mudzadalitsa aliyense wolungama.+Mudzamutchinga ndi chivomerezo chanu+ ngati kuti mukum’teteza ndi chishango chachikulu.+
Mawu a M'munsi
^ “Nehiloti” ndi mawu achiheberi ndipo tanthauzo lake lenileni silikudziwika. N’kutheka kuti ndi dzina la chipangizo choimbira mochita kuuziramo mpweya kapena dzina la nyimbo yoimba motsagana ndi zipangizo zoimbira.
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.