Salimo 4:1-8
Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe.+ Nyimbo ya Davide.
4 Ndikaitana, mundiyankhe inu Mulungu wanga wolungama.+M’masautso anga mundiimiritse pamalo otakasuka.Mundikomere mtima+ ndipo imvani pemphero langa.
2 Inu ana a anthu, kodi mudzandinyoza chifukwa cha ulemerero wanga+ kufikira liti?Mudzakonda zinthu zopanda pake kufikira liti?Mudzafunafuna nkhani yoti mundinamizire kufikira liti? [Seʹlah.]
3 Choncho dziwani kuti Yehova adzapatula wokhulupirika wake.+Yehova adzamva ndikaitana.+
4 Ngati mwakwiya, musachimwe.+Lankhulani mumtima mwanu, muli pabedi panu,+ ndipo mukhale chete. [Seʹlah.]
5 Perekani nsembe zachilungamo,+Ndipo khulupirirani Yehova.+
6 Pali ambiri amene akunena kuti: “Ndani adzationetsa zinthu zabwino?”Inu Yehova, tiunikeni ndi kuwala kwa nkhope yanu.+
7 Mudzasangalatsadi mtima wanga,+Kuposanso mmene iwo amasangalalira, mbewu ndi vinyo wawo watsopano zikachuluka.+
8 Ndidzagona pansi ndi kupeza tulo mu mtendere,+Pakuti inu nokha Yehova mumandichititsa kukhala wotetezeka.+