Salimo 133:1-3
Nyimbo ya Davide Yokwerera Kumzinda.
133 Taonani! Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambiriAbale akakhala pamodzi mogwirizana!+
2 Zili ngati mafuta abwino amene athiridwa pamutu,+Amene akutsikira kundevu,Ndevu za Aroni,+Amenenso akuyenderera mpaka m’khosi la zovala zake.+
3 Zili ngati mame+ a ku Herimoni,+Amene akutsikira pamapiri a ku Ziyoni.+Pakuti Yehova analamula dalitso kukhala kumeneko,+Walamulanso kuti kukhale moyo mpaka kalekale.+