Salimo 76:1-12
Kwa wotsogolera nyimbo: Iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+
76 Mulungu amadziwika mu Yuda.+Dzina lake ndi lalikulu mu Isiraeli.+
2 Malo ake opumulirako ali ku Salemu,+Malo ake okhalamo ali ku Ziyoni.+
3 Kumeneko wathyola mivi yoyaka moto,+Wathyola chishango, lupanga ndi zida zankhondo.+ [Seʹlah.]
4 Inu Mulungu, mwazunguliridwa ndi kuwala, ndipo ndinu wochititsa nthumanzi kuposa mapiri amene muli nyama zodya zinzake.+
5 Anthu olimba mtima alandidwa zinthu zawo,+Iwo awodzera ndi kugona tulo,+Ndipo palibe ngakhale mmodzi mwa anthu onse olimba mtimawo amene ali ndi mphamvu zotsutsa.+
6 Hatchi komanso wokwera galeta agona tulo tofa nato chifukwa cha kudzudzula kwanu, inu Mulungu wa Yakobo.+
7 Inu ndinu wochititsa mantha,+Ndani angaime pamaso panu inu mutakwiya kwambiri?+
8 Munachititsa ziweruzo zanu kumveka kuchokera kumwambako.+Dziko lapansi linachita mantha ndipo linakhala duu+
9 Pamene Mulungu ananyamuka ndi kupereka chiweruzo,+Kuti apulumutse anthu onse ofatsa padziko lapansi.+ [Seʹlah.]
10 Pakuti mkwiyo wa munthu udzakutamandani,+Mkwiyo wake wotsala mudzaumangirira m’chiuno mwanu.
11 Inu nonse amene mwazungulira Mulungu, lonjezani ndi kukwaniritsa malonjezo anuwo kwa Yehova Mulungu wanu.+Bweretsani mphatso mwamantha.+
12 Mulungu adzatsitsa atsogoleri odzikuza.+Iye ndi wochititsa mantha kwa mafumu a padziko lapansi.+