Salimo 60:1-12
Kwa wotsogolera nyimbo pa Duwa la Chikumbutso. Mikitamu.* Salimo la Davide. Nyimbo yophunzitsira.+ Pa nthawi imene Davide anali pankhondo ndi Aramu-naharaimu ndi Aramu-Zoba, ndipo Yowabu anabwerera ndi kukapha Aedomu 12,000 m’chigwa cha Mchere.+
60 Inu Mulungu, mwatitaya, ndipo mwasokoneza magulu athu ankhondo,+Mwakwiya. Tiloleni tibwerere kwa inu.+
2 Mwagwedeza dziko lapansi, ndipo mwaling’amba.+Tsekani ming’alu yake, pakuti lagwedezeka.+
3 Anthu anu mwawaonetsa zovuta.+Mwatimwetsa vinyo ndipo tikuyenda dzandidzandi.+
4 Anthu okuopani mwawapatsa chizindikiro+Kuti athawe uta mokhotakhota. [Seʹlah.]
5 Kuti okondedwa anu apulumutsidwe,+Tipulumutseni ndi dzanja lanu lamanja ndi kutiyankha.+
6 Pokhala woyera, Mulungu walankhula kuti:+“Ndidzakondwa ndi kupereka Sekemu ngati gawo la cholowa.+Ndipo ndidzayezera anthu anga chigwa cha Sukoti.+
7 Giliyadi ndi wanga ndipo Manase ndi wanganso.+Efuraimu ndi malo otetezeka a mtsogoleri amene ine ndamuika.Yuda ndi ndodo ya mtsogoleri wanga.+
8 Mowabu ndi beseni langa losambiramo.+Ndidzaponyera Edomu nsapato zanga.+Ndidzafuula mosangalala chifukwa chogonjetsa Filisitiya.”+
9 Ndani adzandibweretsa kumzinda wozunguliridwa ndi adani?+Ndani adzanditsogolera mpaka kukafika ku Edomu?+
10 Ndinu Mulungu amene mungatichititse kupambana! Koma onani tsopano mwatitaya,+Ndipo inu Mulungu wathu, simukupita kunkhondo pamodzi ndi magulu athu ankhondo.+
11 Tithandizeni kuti tichoke m’masautso,+Pakuti chipulumutso chochokera kwa munthu wochokera kufumbi n’chopanda pake.+
12 Ndi thandizo la Mulungu, tidzalandira mphamvu,+Ndipo Mulungu adzapondereza adani athu.+