Salimo 92:1-15

Nyimbo ndi Salimo la pa tsiku la sabata. 92  Ndi bwino kuyamika inu Yehova,+Ndi kuimba nyimbo zotamanda dzina lanu, inu Wam’mwambamwamba.+   Ndi bwino kunena za kukoma mtima kwanu kosatha m’mawa,+Ndi za kukhulupirika kwanu usiku,+   Ndipo ndidzatero pogwiritsa ntchito choimbira cha zingwe 10 ndi choimbira cha zingwe zitatu.+Ndidzaimba nyimbo yomveka bwino ndi zeze.+   Pakuti mwandichititsa kusangalala, inu Yehova, chifukwa cha zochita zanu.Ndimafuula mosangalala chifukwa cha ntchito ya manja anu.+   Ntchito zanu ndi zazikuludi inu Yehova!+Maganizo anu ndi ozama kwambiri.+   Munthu wopanda nzeru sangadziwe zimenezi,+Ndipo munthu wopusa sangazimvetse.+   Anthu oipa akamaphuka ngati msipu,+Ndipo anthu onse ochita zopweteka anzawo akamaphuka ngati maluwa,Amatero kuti awonongeke kwamuyaya.+   Koma inu Yehova, ndinu wokwezeka mpaka kalekale.+   Pakuti taonani adani anu, inu Yehova!+Adani anu onse adzatha!+Anthu onse ochita zopweteka anzawo adzamwazikana.+ 10  Koma inu mudzakweza nyanga* yanga ngati nyanga ya ng’ombe yam’tchire yamphongo.*+Ndidzadzola mafuta abwino.+ 11  Diso langa lidzayang’ana adani anga atagonja,+Makutu anga adzamva za anthu ondiukira, anthu ochita zoipa. 12  Wolungama adzakula ngati mtengo wa kanjedza,+Ndipo adzakula kwambiri ngati mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni.+ 13  Anthu obzalidwa m’nyumba ya Yehova,+M’mabwalo a Mulungu wathu,+ adzakula mosangalala. 14  Zinthu zidzapitiriza kuwayendera bwino ngakhale atachita imvi,+Adzakhalabe onenepa ndi athanzi,+ 15  Kuti alengeze kuti Yehova ndi wolungama.+Iye ndi Thanthwe langa,+ ndipo sachita zosalungama.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.
Mwina nyama imeneyi inali yooneka ngati njati.