Salimo 124:1-8

Nyimbo ya Davide Yokwerera Kumzinda. 124  “Yehova akanapanda kukhala kumbali yathu,”+Isiraeli anene kuti,+   “Yehova akanapanda kukhala kumbali yathu,+Pamene anthu anatiukira,+   Akanatimeza amoyo,+Pamene mkwiyo wawo unatiyakira.+   Pamenepo madzi akanatikokolola,+Mtsinje wamphamvu ukanatimiza.+   Madzi amphamvuAkanatimiza.+   Yehova atamandike, chifukwa sanatipereke kwa iwo+Kuti atikhadzule ngati nyama.+   Moyo wathu uli ngati mbalame imene yathawa+Pamsampha wa munthu wogwiritsa ntchito nyambo.+Msamphawo wathyoka,+Ndipo ife tapulumuka.+   Thandizo lathu lili m’dzina la Yehova,+Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi.”+

Mawu a M'munsi