Salimo 109:1-31
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la Davide.
109 Inu Mulungu amene ndimakutamandani,+ musakhale chete.+
2 Munthu woipa ndiponso munthu wachinyengo andinenera zoipa ndi pakamwa pawo.+Iwo anena za ine ndi lilime lonama.+
3 Andizungulira ndi mawu achidani,+Ndipo akulimbana nane popanda chifukwa.+
4 Ndikawasonyeza chikondi amanditsutsa,+Koma ine ndimapemphera.+
5 Ndikawachitira zabwino amandibwezera zoipa,+Ndikawasonyeza chikondi amandibwezera chidani.+
6 Muikireni woweruza woipa,Ndipo kudzanja lake lamanja kuime wotsutsana naye.+
7 Pamene akuweruzidwa amuweruze kuti ndi woipa.Ndipo pemphero lake likhale tchimo.+
8 Masiku a moyo wake akhale ochepa.+Udindo wake monga woyang’anira utengedwe ndi munthu wina.+
9 Ana ake akhale amasiye,*+Ndipo mkazi wakenso akhale wamasiye.+
10 Ana ake azingoyendayenda ndithu,+Ndipo azipemphapempha.Azichoka m’mabwinja mmene akukhala, n’kupita kukafunafuna chakudya.+
11 Wopereka ngongole yakatapira* atchere msampha pa zonse zimene ali nazo,+Ndipo anthu achilendo+ afunkhe zinthu zimene wakhetsera thukuta.+
12 Pasapezeke womusonyeza kukoma mtima kosatha,+Ndipo pasapezeke wokomera mtima ana ake amasiyewo.
13 Mbadwa zake ziphedwe ndi kuchotsedwa m’dziko.+Dzina lawo lifafanizidwe mu m’badwo wotsatira.+
14 Yehova akumbukire cholakwa cha makolo ake,+Ndipo tchimo la mayi ake+ lisafafanizidwe.+
15 Tchimo ndi cholakwacho zikhale pamaso pa Yehova nthawi zonse,+Ndipo achotse dzina lawo padziko lapansi kuti lisakumbukiridwenso,+
16 Chifukwa chakuti sanakumbukire kusonyeza kukoma mtima kosatha,+M’malomwake anapitiriza kuthamangitsa wosautsika ndi wosauka,+Komanso munthu wa mtima wachisoni kuti amuphe.+
17 Iye anakonda kutemberera ena,+ mwakuti matemberero anabwera kwa iye.+Koma kudalitsa ena sikunali kumusangalatsa,+Moti madalitso anali patali ndi iye,+
18 Iye anali kuvala matemberero ngati chovala.+Matembererowo analowa mwa iye ngati madzi,+Ndiponso analowa m’mafupa ake ngati mafuta.
19 Kwa iye matembererowo akhale ngati chovala chimene amadziphimba nacho,+Komanso ngati lamba amene amamanga m’chiuno mwake nthawi zonse.+
20 Amenewa ndi malipiro a Yehova kwa aliyense amene amalimbana nane,+Ndi kwa amene amakamba zondichitira zinthu zoipa.+
21 Koma inu ndinu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa.+Ndikomereni mtima chifukwa cha dzina lanu.+Ndilanditseni,+ popeza kukoma mtima kwanu kosatha ndi kwakukulu.
22 Ine ndasautsika ndipo ndasauka,+Mtima wanga walasika mkati mwanga.+
23 Ine ndiyenera kuchoka mofanana ndi chithunzithunzi chimene chimazimiririka dzuwa likalowa.+Ndakutumulidwa ngati dzombe.
24 Mawondo anga akugwedezeka chifukwa chosala kudya,+Ndawonda ndipo ndilibe mafuta alionse odzola.+
25 Kwa iwo ndakhala chinthu choyenera kutonzedwa.+Akandiona amapukusa mitu yawo.+
26 Ndithandizeni, inu Yehova Mulungu wanga.+Ndipulumutseni malinga ndi kukoma mtima kwanu kosatha.+
27 Iwo adziwe kuti ili ndi dzanja lanu.+Adziwe kuti inu Yehova mwachita zimenezi.+
28 Alekeni anditemberere,+Koma inu mundipatse madalitso.+Iwo aimirira kuti andiukire koma inu muwachititse manyazi,+Ndipo ine mtumiki wanu ndisangalale.+
29 Amene akulimbana ndi ine avale manyazi,+Ndipo adziphimbe ndi manyaziwo ngati akudziphimba ndi malaya akunja odula manja.+
30 Ndidzatamanda kwambiri Yehova ndi pakamwa panga,+Ndipo ndidzamutamanda pakati pa anthu ambiri.+
31 Pakuti adzaima kudzanja lamanja la munthu wosauka,+Kuti am’pulumutse kwa omuweruza mopanda chilungamo.