Salimo 149:1-9
149 Tamandani Ya, anthu inu!+Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,+Muimbireni nyimbo zomutamanda mu mpingo wa anthu ake okhulupirika.+
2 Isiraeli asangalale ndi Womupanga Wamkulu,+Ana a Ziyoni akondwere ndi Mfumu yawo.+
3 Atamande dzina lake mwa kuvina.+Amuimbire nyimbo zomutamanda ndi maseche ndi zeze,+
4 Pakuti Yehova amasangalala ndi anthu ake.+Iye amakongoletsa anthu ofatsa ndi chipulumutso.+
5 Anthu okhulupirika akondwere mu ulemerero.Iwo aimbe mosangalala pamabedi awo.+
6 Pakamwa pawo patuluke nyimbo zotamanda Mulungu,+Ndipo lupanga lakuthwa konsekonse likhale m’manja mwawo,+
7 Kuti abwezere anthu a mitundu ina,+Ndi kudzudzula mitundu ya anthu,+
8 Ndiponso kuti amange mafumu awo maunyolo,+Ndi kumanga anthu awo olemekezeka m’matangadza achitsulo.
9 Kuti awaweruze motsatira chigamulo cholembedwa.+Ulemerero umenewu ndi wa anthu onse okhulupirika a Mulungu.+Tamandani Ya, anthu inu!+