Salimo 93:1-5

93  Yehova wakhala mfumu!+Iye wavala ulemerero.+Yehova wavala mphamvu ngati chovala, ndipo wamangirira mphamvuzo m’chiuno mwake.+Dziko lapansi lakhazikika, moti silingagwedezeke.+   Mpando wanu wachifumu unakhazikika kalekale.+Munakhalako kuyambira kalekale.+   Inu Yehova, mitsinje ikufuula.Ikufuula ndi mawu amphamvu.+Mitsinje ikupitiriza kufuula ndi mawu amkokomo.+   Ulemerero wa Yehova ndi waukulu+ kumwamba,Kuposa mkokomo wa madzi ambiri, kuposanso mafunde amphamvu a m’nyanja.+   Zikumbutso zanu ndi zodalirika zedi.+Chiyero ndi choyenera nyumba yanu+ mpaka muyaya, inu Yehova.+

Mawu a M'munsi