Salimo 106:1-48
106 Tamandani Ya, anthu inu!+Yamikani Yehova, chifukwa iye ndi wabwino.+Pakuti kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
2 Ndani anganene zinthu zamphamvu zimene Yehova wachita,+Kapena ndani angamutamande mokwanira?+
3 Odala ndi anthu amene amatsata chilungamo,+Ndi kuchita zolungama nthawi zonse.+
4 Ndikumbukireni inu Yehova, ndipo ndisonyezeni kukoma mtima kumene mumasonyeza anthu anu.+Ndisamalireni ndi kundipulumutsa,+
5 Kuti ndione ubwino umene mumapereka kwa osankhidwa anu,+Kuti ndikondwere pamene mtundu wanu ukukondwera,+Ndiponso kuti ndinyadire pamodzi ndi cholowa chanu.+
6 Tachimwa mofanana ndi makolo athu.+Tachita zinthu zosayenera, tachita zinthu zoipa.+
7 Makolo athu ku Iguputo,Sanasonyeze kuzindikira kulikonse ntchito zanu zodabwitsa.+Sanakumbukire kuchuluka kwa kukoma mtima kwanu kosatha,+Koma anapanduka panyanja, pafupi ndi Nyanja Yofiira.+
8 Koma Mulungu anawapulumutsa chifukwa cha dzina lake,+Kuti mphamvu zake zidziwike.+
9 Choncho anadzudzula Nyanja Yofiira, ndipo pang’onopang’ono nyanjayo inauma.+Pamenepo anawayendetsa kudutsa pakati pa madzi akuya ngati akuwayendetsa m’chipululu.+
10 Chotero anawapulumutsa m’manja mwa wodana nawo,+Ndipo anawawombola m’manja mwa mdani.+
11 Ndiyeno madzi anamiza adani awo,+Moti panalibe ngakhale mmodzi amene anapulumuka.+
12 Pamenepo anakhulupirira mawu ake,+Ndipo anayamba kumuimbira nyimbo zomutamanda.+
13 Koma mofulumira anaiwala ntchito zake,+Iwo sanayembekezere malangizo ake.+
14 Anasonyeza chikhumbo chawo chadyera m’chipululu,+Ndipo anayesa Mulungu m’chipululumo.+
15 Mulungu anawapatsa zimene anali kupempha,+Ndipo anawagwetsera matenda a kaliwondewonde pakati pawo.+
16 Iwo anayamba kuchitira Mose kaduka mumsasa,+Ndiponso Aroni, woyera wa Yehova.+
17 Pamenepo dziko lapansi linatseguka ndipo linameza Datani,+Ndi kufotsera msonkhano wa Abiramu.+
18 Moto unayaka pakati pa msonkhano wawo.+Malawi amoto ananyeketsa anthu oipawo.+
19 Iwo anapanganso mwana wa ng’ombe ku Horebe,+Ndipo anaweramira chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula.+
20 Choncho anasinthanitsa ulemerero wanga+Ndi chifaniziro cha ng’ombe yamphongo yodya udzu.+
21 Iwo anaiwala Mulungu, Mpulumutsi wawo,+Amene anachita zinthu zazikulu ku Iguputo,+
22 Amene anachita zodabwitsa m’dziko la Hamu,+Amene anachita zochititsa mantha pa Nyanja Yofiira.+
23 Iye anangotsala pang’ono kulamula kuti awawononge,+Koma Mose wosankhidwa wake,Anaima pamalo ogumuka pamaso pa Mulungu,+Ndi kubweza mkwiyo wake kuti usawawononge.+
24 Iwo anayamba kunyansidwa ndi dziko losiririka,+Ndipo analibe chikhulupiriro m’mawu ake.+
25 Anapitiriza kung’ung’udza m’mahema awo,+Moti sanamvere mawu a Yehova.+
26 Choncho Mulungu anawalumbirira atakweza dzanja lake,+Kuti adzawapha m’chipululu,+
27 Ndiponso kuti adzachititsa ana awo kuphedwa ndi mitundu ina,+Ndi kuti adzawamwaza m’mayiko osiyanasiyana.+
28 Iwo anayamba kulambira Baala wa ku Peori,+Ndi kudya nsembe zoperekedwa ku zinthu zakufa.+
29 Pamene anali kukhumudwitsa Mulungu chifukwa cha zochita zawo,+Pakati pawo panagwa mliri.+
30 Pinihasi ataimirira ndi kuchitapo kanthu,+Mliriwo unatha.
31 Ndipo Pinihasi anaonedwa kukhala wolungamaKu mibadwomibadwo mpaka kalekale.+
32 Kuwonjezera pamenepo, iwo anaputa mkwiyo pa madzi a ku Meriba,+Moti Mose sizinamuyendere bwino chifukwa cha anthu amenewa.+
33 Iwo anamukwiyitsaNdipo Mose anayamba kulankhula mosalingalira bwino.+
34 Iwowa sanawononge mitundu ina ya anthu,+Mmene Yehova anawauzira.+
35 Iwo anayamba kusakanikirana ndi mitundu ina,+Ndi kuyamba kuphunzira zochita zawo.+
36 Anayamba kutumikira mafano awo,+Ndipo mafanowo anakhala msampha wawo.+
37 Anali kupereka nsembe ana awo aamuna+Ndi ana awo aakazi kwa ziwanda.+
38 Choncho anali kukhetsa magazi a anthu osalakwa,+Magazi a ana awo aamuna ndi a ana awo aakazi,Amene anawapereka nsembe kwa mafano a ku Kanani.+Ndipo dzikolo linaipa ndi magazi amene iwo anakhetsa.+
39 Iwo anakhala odetsedwa chifukwa cha ntchito zawo,+Zochita zawo zinawalowetsa m’makhalidwe oipa.+
40 Mkwiyo wa Yehova unayamba kuyakira anthu ake,+Ndipo iye ananyansidwa ndi cholowa chake.+
41 Mobwerezabwereza anali kuwapereka m’manja mwa anthu a mitundu ina,+Kuti anthu odana nawo awalamulire,+
42 Ndi kuti adani awowo awapondereze,Komanso kuti awagonjetse.+
43 Nthawi zambiri anali kuwalanditsa,+Koma iwo anali kumupandukira chifukwa sanali kumumvera,+Ndipo anali kuwatsitsa chifukwa cha zolakwa zawo.+
44 Mulungu akamva kuchonderera kwawo+Anali kuona kuvutika kwawo.+
45 Zikatero anali kukumbukira pangano limene anachita ndi iwo,+Ndipo anali kuwamvera chisoni chifukwa cha kuchuluka kwa kukoma mtima kwake kosatha.+
46 Ndipo anali kuchititsa kuti anthu onse owagwira ukapoloAwamvere chisoni.+
47 Tipulumutseni inu Yehova Mulungu wathu,+Tisonkhanitseni pamodzi kuchokera m’mitundu ina,+Kuti titamande dzina lanu loyera,+Ndi kuti tilankhule mokondwa pokutamandani.+
48 Adalitsike Yehova Mulungu wa Isiraeli,+Kuyambira kalekale mpaka kalekale.Ndipo anthu onse anene kuti, Ame.*+Tamandani Ya, anthu inu!+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti “Zikhale momwemo!”