Salimo 121:1-8
Nyimbo Yokwerera Kumzinda.
121 Ndakweza maso anga kuyang’ana kumapiri.+Kodi thandizo langa lichokera kuti?+
2 Thandizo langa lichokera kwa Yehova,+Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi.+
3 Iye sangalole kuti phazi lako lipunthwe.+Amene amakuyang’anira sangawodzere.+
4 Taonani! Amene akuyang’anira Isiraeli,+Sangawodzere kapena kugona.+
5 Yehova akukuyang’anira.+Yehova ndiye mthunzi wako+ kudzanja lako lamanja.+
6 Masana dzuwa silidzakupweteka,+Kapenanso mwezi usiku.+
7 Yehova adzakuteteza ku masoka onse.+Iye adzateteza moyo wako.+
8 Yehova adzakuteteza pa zochita zako zonse,+Kuyambira tsopano mpaka kalekale.+