Salimo 95:1-11

95  Bwerani tifuule kwa Yehova mokondwera!+Iye amene ndi Thanthwe la chipulumutso chathu, timufuulire mosangalala chifukwa wapambana.+   Tiyeni tionekere pamaso pake ndi chiyamiko.+Tiyeni tiimbe nyimbo zomutamanda ndi kumufuulira mosangalala chifukwa wapambana.+   Pakuti Yehova ndi Mulungu wamkulu,+Ndiponso ndi Mfumu yaikulu kuposa milungu ina yonse.+   Malo ozama kwambiri a dziko lapansi ali m’manja mwake,+Mapiri aatali nawonso ndi ake.+   Nyanja imene anapanga ndi yake,+Iye amenenso anapanga mtunda ndi manja ake.+   Bwerani timuweramire ndi kumupembedza.+Tiyeni tigwade+ pamaso pa Yehova amene ndiye Wotipanga.+   Pakuti iye ndi Mulungu wathu ndipo ife ndife anthu ake. Iye amatisamalira ngati nkhosa zimene akuweta.+Lero anthu inu mukamvera mawu a Mulungu,+   Musaumitse mitima yanu monga mmene makolo anu anachitira pa Meriba,+Monga mmene anachitira pa Masa m’chipululu,+   Pamene makolo anu anandiyesa.+Iwo anandisanthula, ndipo anaonanso ntchito zanga.+ 10  Kwa zaka 40, m’badwo umenewo unali kundinyansa,+Ndipo ndinati:“Anthu awa mitima yawo imasochera,+Ndipo sadziwa njira zanga.”+ 11  Kunena za anthu amenewa ndinalumbira mu mkwiyo wanga kuti:+“Sadzalowa mu mpumulo wanga.”+

Mawu a M'munsi