Salimo 142:1-7
Masikili.* Salimo ndiponso pemphero la Davide, pamene anali kukhala kuphanga.+
142 Ndinafuulira Yehova kuti andithandize.+Ndinafuulira Yehova kuti andikomere mtima.+
2 Ndinapitirizabe kumukhuthulira nkhawa zanga.+Ndinapitirizabe kumuuza masautso anga.+
3 Ndinachita zimenezi pamene mtima wanga+ unalefuka.Pamenepo, munadziwa njira yanga.+Adani anga anditchera msampha+M’njira imene ndikuyenda.+
4 Yang’anani kudzanja lamanja ndipo muoneKuti palibe aliyense amene akufuna kundithandiza.+Ndilibenso malo othawirako,+Ndipo palibe amene akufunsa za moyo wanga.+
5 Ndinafuula kwa inu kuti mundithandize, inu Yehova.+Ndinanena kuti: “Inu ndinu pothawirapo panga,+Gawo langa+ m’dziko la amoyo.”+
6 Mvetserani kulira kwanga kochonderera,+Pakuti ndasautsika koopsa.+Ndipulumutseni kwa anthu amene akundizunza,+Pakuti iwo ndi amphamvu kuposa ine.+
7 Nditulutseni mundende ya mdima+Kuti nditamande dzina lanu.+Chititsani kuti anthu olungama asonkhane ndi kundizungulira,+Chifukwa mumandichitira zabwino.+