Salimo 104:1-35

104  Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.+Inu Yehova Mulungu wanga, mwasonyeza kuti ndinu wamkulu koposa.+Mwadziveka ulemu ndi ulemerero.+   Mwadzifunditsa kuwala ngati chofunda,+Mwatambasula kumwamba ngati nsalu ya chihema.+   Inu munamanga zipinda za m’mwamba pamadzi pogwiritsa ntchito mitanda,+Munapanga mitambo kukhala galeta lanu,+Mumayenda pamapiko a mphepo.+   Inu mumapanga angelo anu kukhala mizimu,+Ndipo atumiki anu kukhala moto wonyeketsa.+   Mwakhazikitsa dziko lapansi pamaziko olimba.+Silidzagwedezeka mpaka kalekale, mpaka muyaya.+   Munalikuta ndi madzi ngati mwalikuta ndi nsalu.+Madziwo anakwera kupitirira mapiri.+   Chifukwa cha kudzudzula kwanu, madziwo anayamba kuthawa.+Atamva mabingu anu anayamba kuthamanga mopanikizika kwambiri,   Kupita kumalo amene munawakonzera.Mapiri anakwera,+Zigwa zinatsika.   Munawaikira malire kuti asapitirire malirewo,+Kuti asamizenso dziko lapansi.+ 10  Mwatsegula akasupe m’zigwa,+Ndipo madziwo akudutsa pakati pa mapiri. 11  Akasupewo amapereka madzi kwa zilombo zonse zakutchire.+Nthawi zonse mbidzi+ zimapha ludzu lawo mmenemo. 12  Zolengedwa zouluka m’mlengalenga zimamanga zisa zawo pafupi ndi akasupewo,+Ndipo zimalira m’mitengo ya masamba ambiri obiriwira.+ 13  Mulungu amathirira mapiri kuchokera m’zipinda zake za m’mwamba.+Dziko lapansi ladzaza ndi zipatso za ntchito yake.+ 14  Amameretsa msipu kuti nyama zidye,+Ndipo amameretsa mbewu kuti anthu agwiritse ntchito.+Amachita zimenezi kuti chakudya chituluke m’nthaka,+ 15  Komanso kuti mutuluke vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu.+Amachita zonsezi kuti nkhope ya munthu isalale ndi mafuta,+Komanso kuti apereke chakudya chimene chimakhutiritsa mtima wa munthu.+ 16  Mitengo ya Yehova imathiriridwa bwino,Mikungudza ya ku Lebanoni imene iye anabzala.+ 17  Mbalame zimamanga zisa zawo mmenemo.+Dokowe nyumba yake ndiyo mitengo ya mlombwa.+ 18  M’mapiri aatali+ ndi mmene mumakhala mbuzi zakumapiri.+Ndipo m’mapanga ndiye mothawiramo mbira.+ 19  Wapanga mwezi kuti uzisonyeza nthawi yoikidwiratu.+Dzuwa nalo limadziwa bwino kumene limalowera.+ 20  Munapanga mdima kuti kukhale usiku.+Nyama zonse zakutchire zimayendayenda usikuwo. 21  Mkango wamphamvu umabangula pofunafuna nyama,+Ndiponso popempha chakudya kwa Mulungu.+ 22  Dzuwa likayamba kuwala+ zimachoka,Ndipo zimakagona m’malo awo obisalamo. 23  Munthu amapita ku ntchito zake,+Ndipo amagwira ntchito mpaka madzulo.+ 24  Ntchito zanu ndi zochuluka, inu Yehova!+Zonsezo munazipanga mwanzeru zanu.+Dziko lapansi ladzaza ndi zinthu zimene munapanga.+ 25  M’nyanja yakuya iyi ndiponso yotambalala,+Muli zinthu zoyenda zosawerengeka,+Muli zamoyo zazikulu ndi zazing’ono zomwe.+ 26  Zombo zimayenda mmenemo.+Ndipo Leviyatani*+ munam’panga kuti azisewera mmenemo.+ 27  Zonsezi zimayembekezera inu+Kuti muzipatse chakudya pa nyengo yake.+ 28  Zimalandira zimene mwazipatsa.+Mumatambasula dzanja lanu ndipo zimakhutira ndi zinthu zabwino.+ 29  Mukaphimba nkhope yanu, zimasokonezeka.+Mukachotsa mzimu wawo, zimafa,+Ndipo zimabwerera kufumbi.+ 30  Mukatumiza mzimu wanu zimalengedwa.+Ndipo mumachititsa dziko kukhala latsopano. 31  Ulemerero wa Yehova udzakhalapobe mpaka kalekale.+Yehova adzakondwera ndi ntchito zake.+ 32  Amayang’ana dziko lapansi ndipo limanjenjemera.+Amagwira mapiri ndipo amafuka utsi.+ 33  Ndidzaimbira Yehova moyo wanga wonse.+Ndidzaimba nyimbo zotamanda Mulungu wanga nthawi yonse ya moyo wanga.+ 34  Kulingalira za iye kukhale kosangalatsa.+Ine ndidzakondwera mwa Yehova.+ 35  Ochimwa adzafafanizidwa padziko lapansi.+Ndipo anthu oipa sadzakhalaponso.+Tamanda Yehova, iwe moyo wanga. Tamandani Ya, anthu inu!*+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “ng’ona.”
Kapena kuti “Aleluya.”