Salimo 33:1-22
33 Fuulani mosangalala chifukwa cha Yehova, inu nonse olungama.+M’poyenera kuti owongoka mtima atamande Mulungu.+
2 Yamikani Yehova poimba zeze.+Muimbireni nyimbo zomutamanda ndi choimbira cha zingwe 10.+
3 Muimbireni nyimbo yatsopano.+Muimbireni choimbira cha zingwe ndi mtima wonse ndi kufuula mosangalala.+
4 Pakuti mawu a Yehova ndi owongoka,+Ndipo ntchito zake zonse ndi zodalirika.+
5 Iye amakonda chilungamo ndi chiweruzo chosakondera.+Dziko lapansi ladzaza ndi kukoma mtima kosatha kwa Yehova.+
6 Kumwamba kunalengedwa ndi mawu a Yehova,+Ndipo makamu ake onse analengedwa ndi mpweya wa m’kamwa mwake.+
7 Anasonkhanitsa madzi a m’nyanja ngati wachita kuwatchinga ndi khoma,+Anaika madzi amphamvu m’nyumba zosungiramo zinthu.
8 Onse okhala padziko lapansi aope Yehova.+Anthu onse okhala panthaka ya dziko lapansi achite naye mantha.+
9 Pakuti iye ananena, ndipo zinachitika.+Iye analamula, ndipo zinakhalapo.+
10 Yehova wasokoneza zolinga za anthu a mitundu ina.+Walepheretsa maganizo a mitundu ya anthu.+
11 Zolinga za Yehova zidzakhalapo mpaka kalekale.+Maganizo a mumtima mwake adzakhalapo ku mibadwomibadwo.+
12 Wodala ndi mtundu umene Mulungu wawo ndi Yehova,+Anthu amene iye wawasankha kukhala cholowa chake.+
13 Kuchokera kumwamba, Yehova wayang’ana,+Waona ana onse a anthu.+
14 Kuchokera kumalo achikhalire kumene iye amakhala,+Wayang’anitsitsa onse okhala padziko lapansi.
15 Iye akuumba mtima wa aliyense wa iwo.+Akulingalira ntchito zawo zonse.+
16 Palibe mfumu imene inapulumuka chifukwa cha kukula kwa gulu lake lankhondo.+Munthu wamphamvu sapulumuka chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zake.+
17 Hatchi siingabweretse chipulumutso,+Siingapulumutse munthu chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zake.+
18 Taonani! Diso la Yehova lili pa anthu amene amamuopa,+Amene amayembekezera kukoma mtima kwake kosatha,+
19 Kuti apulumutse moyo wawo ku imfa,+Ndi kuwasunga ndi moyo pa nthawi ya njala.+
20 Moyo wathu wakhala ukuyembekeza Yehova.+Iye ndi mthandizi wathu ndi chishango chathu.+
21 Mitima yathu imakondwera mwa iye.+Pakuti timadalira dzina lake loyera.+
22 Inu Yehova, kukoma mtima kwanu kosatha kukhale pa ife,+Pakuti takhala tikuyembekezera inu.+