Salimo 94:1-23

94  Inu Yehova, Mulungu wobwezera anthu oipa,+Inu Mulungu wobwezera anthu oipa, walani!+   Nyamukani inu Woweruza dziko lapansi.+Perekani chilango kwa anthu odzikweza.+   Kodi anthu oipa adzakondwera kufikira liti?+Kodi adzakondwera kufikira liti, inu Yehova?+   Iwo amalankhula zopanda pake, ndipo amalankhula mosasamala.+Onse ochita zopweteka anzawo amadzitukumula.+   Iwo amaphwanya anthu anu, inu Yehova,+Ndipo amasautsa cholowa chanu.+   Amapha mkazi wamasiye ndi mlendo wokhala m’dziko lawo,+Ndipo amaphanso ana amasiye.*+   Iwo amanena kuti: “Ya sakuona,+Ndipo Mulungu wa Yakobo sakudziwa zimene zikuchitika.”+   Zindikirani anthu opanda nzeru inu.+Ndipo opusa inu, mudzakhala liti ozindikira?+   Kodi amene anakupatsani makutu, sangamve?+Kapena amene anapanga maso, sangaone?+ 10  Kodi amene amalangiza mitundu ya anthu,+Amene amaphunzitsa anthu kuti akhale ozindikira, sangathe kudzudzula?+ 11  Yehova amadziwa kuti maganizo a anthu ali ngati mpweya wotuluka m’mphuno.+ 12  Wodala ndi munthu wamphamvu amene inu Ya mumamudzudzula,+Komanso amene inu mumamuphunzitsa chilamulo chanu,+ 13  Kuti mum’patse mtendere pa nthawi ya masoka,+Kufikira dzenje la munthu woipa litakumbidwa.+ 14  Yehova sadzataya anthu ake,+Kapena kusiya cholowa chake.+ 15  Pakuti zigamulo zidzayambiranso kukhala zachilungamo,+Ndipo onse owongoka mtima adzazitsatira. 16  Ndani adzanyamuka kuti amenye nkhondo ndi anthu ochita zoipa m’malo mwa ine?+Ndani adzaima m’malo mwa ine kulimbana ndi anthu ochita zopweteka anzawo?+ 17  Yehova akanapanda kundithandiza,+Ndikanatsikira kuli chete mofulumira.+ 18  Pamene ndinanena kuti: “Phazi langa literereka,”+Kukoma mtima kwanu kosatha, inu Yehova, kunandichirikiza.+ 19  Malingaliro osautsa atandichulukira mumtima mwanga,+Mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.+ 20  Kodi inu mudzagwirizana ndi olamulira ankhanza,+Pamene akuyambitsa mavuto mwa kupanga malamulo?+ 21  Iwo amaukira koopsa munthu wolungama,+Ndipo munthu wosalakwa amamuweruza kuti ndi woipa. Amachita zimenezi kuti akhetse magazi ake.+ 22  Koma Yehova adzakhala malo anga okwezeka ndiponso achitetezo,+Ndipo Mulungu wanga adzakhala thanthwe langa lothawirako.+ 23  Iye adzawabwezera zoipa zawo,+Ndipo adzawakhalitsa chete mwa kuwadzetsera masoka okonza okha.+Yehova Mulungu wathu adzawakhalitsa chete.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “ana aamuna opanda bambo.”