Salimo 14:1-7
Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide.
14 Wopusa amanena mumtima mwake kuti:“Kulibe Yehova.”+Anthu oterewa amachita zoipa,+ ndipo amachita zinthu zonyansa.Palibe amene akuchita zabwino.+
2 Koma kuchokera kumwamba, Yehova wayang’ana ana a anthu padziko lapansi,+Kuti aone ngati pali aliyense wozindikira, aliyense amene akufunafuna Yehova.+
3 Onse apatuka,+ ndipo onsewo ndi achinyengo.+Palibe aliyense amene akuchita zabwino,+Palibiretu ndi mmodzi yemwe.+
4 Kodi palibe aliyense wozindikira mwa anthu ochita zopweteka anzawowa,+Amene akudya anthu anga ngati chakudya?+Iwo sanaitane pa Yehova.+
5 Nthawi yomweyo anagwidwa ndi mantha aakulu,+Pakuti Yehova ali pakati pa khamu* la anthu olungama.+
6 Anthu inu mumanyazitsa malangizo a munthu wosautsika,Chifukwa Yehova ndiye pothawirapo pake.+
7 Haa! Zikanakhala bwino m’Ziyoni mukanapezeka chipulumutso cha Isiraeli.+Yehova akadzasonkhanitsa ndi kubwezeretsa anthu ake amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,+Yakobo adzasangalale, Isiraeli adzakondwere.+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “m’badwo.”