Salimo 113:1-9
113 Tamandani Ya, anthu inu!+Inu atumiki a Yehova, mutamandeni,+Tamandani dzina la Yehova.+
2 Dzina la Yehova lidalitsike,+Kuyambira tsopano mpaka kalekale.+
3 Kuyambira kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera,+Dzina la Yehova liyenera kutamandidwa.+
4 Yehova wakwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.+Ulemerero wake uli pamwamba pa kumwamba.+
5 Ndani angafanane ndi Yehova Mulungu wathu,+Amene amakhala pamwamba?+
6 Iye amatsika m’munsi kuti aone kumwamba ndi dziko lapansi.+
7 Amadzutsa munthu wonyozeka kumuchotsa m’fumbi.+Amakweza munthu wosauka kumuchotsa padzala,+
8 Kuti amukhazike pamodzi ndi anthu olemekezeka,+Pamodzi ndi anthu olemekezeka pakati pa anthu a Mulungu.+
9 Akuchititsa mkazi wosabereka kukhala m’nyumba+Monga mayi wosangalala wa ana aamuna.+Tamandani Ya, anthu inu!+