Salimo 143:1-12

Nyimbo ya Davide. 143  Inu Yehova, imvani pemphero langa.+Tcherani khutu pamene ndikuchonderera.+Ndiyankheni mogwirizana ndi kukhulupirika kwanu ndi chilungamo chanu.+   Musandiimbe mlandu ine mtumiki wanu,+Pakuti palibe aliyense wamoyo amene angakhale wolungama pamaso panu.+   Mdani akufunafuna moyo wanga,+Iye waupondaponda pafumbi.+Wandichititsa kukhala m’malo a mdima ngati anthu amene anafa kalekale.+   Mtima wanga+ walefuka,Ndipo wachita dzanzi.+   Ndakumbukira masiku akale.+Ndasinkhasinkha zochita zanu zonse,+Ndipo ndakhala ndikuganizira ntchito ya manja anu ndi mtima wonse.+   Ine ndikupemphera nditakweza manja anga kwa inu.+Moyo wanga uli ngati dziko louma limene likulakalaka kuti muthetse ludzu lake.+ [Seʹlah.]   Fulumirani, ndiyankheni inu Yehova.+Mphamvu zanga zatha.+Musandibisire nkhope yanu,+Chifukwa mukatero ndikhala ngati anthu amene akutsikira kudzenje la manda.+   M’mawa ndichititseni kumva za kukoma mtima kwanu kosatha,+Pakuti ndimadalira inu.+Ndidziwitseni njira imene ndiyenera kuyendamo,+Pakuti ndapereka moyo wanga kwa inu.+   Ndilanditseni kwa adani anga, inu Yehova.+Ine ndathawira kwa inu.+ 10  Ndiphunzitseni kuchita chifuniro chanu,+Pakuti inu ndinu Mulungu wanga.+Mzimu wanu ndi wabwino.+Unditsogolere m’dziko la olungama.+ 11  Inu Yehova, ndisungenibe wamoyo+ chifukwa cha dzina lanu.+Chotsani moyo wanga m’masautso+ monga mwa chilungamo chanu.+ 12  Adani anga muwakhalitse chete monga mwa kukoma mtima kwanu kosatha.+Ndipo muwononge onse ondichitira zoipa,+Pakuti ine ndine mtumiki wanu.+

Mawu a M'munsi