Salimo 66:1-20
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo.
66 Inu anthu nonse padziko lapansi, fuulirani Mulungu mosangalala chifukwa wapambana.+
2 Imbani nyimbo zotamanda dzina lake.+M’patseni ulemerero ndi kumutamanda.+
3 Muuzeni Mulungu kuti: “Ntchito zanu ndi zochititsadi mantha!+Chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zanu, adani anu adzabwera kwa inu mogonjera.+
4 Anthu onse padziko lapansi adzakugwadirani,+Ndipo adzaimba nyimbo zokutamandani, adzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”+ [Seʹlah.]
5 Bwerani anthu inu, kuti muone ntchito za Mulungu.+Zimene wachitira ana a anthu ndi zochititsa mantha.+
6 Anasandutsa nyanja kukhala malo ouma,+Anthu anawoloka mtsinje mwa kuyenda ndi mapazi awo.+Pamenepo tinayamba kusangalala mwa iye.+
7 Iye akulamulira ndi mphamvu zake mpaka kalekale.+Maso ake akuyang’anitsitsa mitundu ya anthu.+Koma anthu oumitsa khosi asadzikweze.+ [Seʹlah.]
8 Tamandani Mulungu wathu, inu mitundu ya anthu,+Chititsani mawu omutamanda kumveka.+
9 Iye amatisunga ndi moyo,+Ndipo sanalole phazi lathu kupunthwa.+
10 Pakuti inu Mulungu mwatisanthula,+Mwatiyenga ngati siliva.+
11 Mwatilowetsa mu ukonde wosakira nyama,+Mwatinyamulitsa katundu wolemera m’chiuno mwathu.
12 Mwachititsa munthu wamba kutipondaponda.+Tadutsa pamoto ndi pamadzi,+Ndipo inu mwatipatsa mpumulo.+
13 Ndidzalowa m’nyumba yanu ndi nsembe zopsereza zathunthu.+Ine ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa inu+
14 Amene milomo yanga inanena,+Ndiponso amene pakamwa panga pananena nthawi imene ndinali m’masautso aakulu.+
15 Ndidzapereka kwa inu nsembe zathunthu zopsereza za nyama zonenepa,+Pamodzi ndi nsembe zautsi wa nkhosa zamphongo.Ndidzapereka ng’ombe yamphongo pamodzi ndi mbuzi zamphongo.+ [Seʹlah.]
16 Bwerani, mvetserani, inu nonse oopa Mulungu, ndipo ine ndifotokoza+Zimene wandichitira.+
17 Ndinamuitana ndi pakamwa panga,+Ndipo ndinamutamanda ndi lilime langa.+
18 Ngati ndikuganizira choipa chilichonse mumtima mwanga,Yehova sadzandimvera.+
19 Ndithudi, Mulungu wamva,+Wamvetsera mwatcheru mawu a pemphero langa.+
20 Adalitsike Mulungu amene sananyalanyaze pemphero langa,Kapena kundimana kukoma mtima kwake kosatha.+