Salimo 140:1-13
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.
140 Inu Yehova, ndilanditseni kwa anthu oipa.+Nditetezeni kwa munthu wochita zachiwawa,+
2 Anthu amene amakonza chiwembu mumtima mwawo,+Amene amandiukira tsiku lonse ngati mmene zimakhalira pankhondo.+
3 Anola lilime lawo ndipo lakhala ngati la njoka.+M’milomo yawo muli poizoni wa mphiri.+ [Seʹlah.]
4 Inu Yehova, ndithandizeni kuti manja a munthu woipa asandikhudze.+Nditetezeni kwa munthu wochita zachiwawa.+Nditetezeni kwa anthu amene andikonzera chiwembu kuti andikankhe ndi kundigwetsa.+
5 Anthu odzikweza anditchera msampha.+Iwo aika zingwe ponseponse ngati ukonde m’mphepete mwa njira,+Ndipo anditchera makhwekhwe.+ [Seʹlah.]
6 Ndauza Yehova kuti: “Inu ndinu Mulungu wanga.+Tcherani khutu, inu Yehova, ku mawu anga ochonderera.”+
7 Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa,+ mpulumutsi wanga wamphamvu,+Mwatchinga ndi kuteteza mutu wanga pa tsiku lankhondo.+
8 Inu Yehova, munthu woipa musam’patse zimene mtima wake umafuna.+Musalole kuti chiwembu chawo chitheke chifukwa angadzikweze.+ [Seʹlah.]
9 Kunena za anthu amene andizungulira,+Zoipa zotuluka pakamwa pawo ziphimbe mitu yawo.+
10 Muwakhuthulire makala oyaka moto pamutu pawo.+Muwachititse kugwera m’moto+ ndi m’madzi akuya kuti asanyamukenso.+
11 Munthu wolankhula zazikulu* asakhazikike padziko lapansi.+Zoipa zisakesake munthu wochita zachiwawa ndipo zimukanthe mobwerezabwereza.+
12 Ndikudziwa bwino kwambiri kuti Yehova adzazengera+Mlandu anthu osautsika. Iye adzachitira chilungamo anthu osauka.+
13 Ndithudi, anthu olungama adzatamanda dzina lanu.+Anthu owongoka mtima adzakhalabe pamaso panu.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti “woneneza.” Mawu ake enieni ndi “munthu wa lilime.”