Salimo 96:1-13

96  Imbirani Yehova nyimbo yatsopano.+Imbirani Yehova, inu anthu nonse okhala padziko lapansi.+   Imbirani Yehova, tamandani dzina lake.+Tsiku ndi tsiku lengezani uthenga wabwino wa chipulumutso chake.+   Lengezani ulemerero wake pakati pa anthu a mitundu ina,+Ndiponso ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu.+   Pakuti Yehova ndi wamkulu+ ndi woyenera kutamandidwa kwambiri.Iye ndi wochititsa mantha kuposa milungu ina yonse.+   Chifukwa milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi milungu yopanda pake,+Koma Yehova ndiye anapanga kumwamba.+   Ulemu ndi ulemerero zili pamaso pake.+Mphamvu ndi kukongola zili m’nyumba yake yopatulika.+   Vomerezani Yehova, inu mabanja a mitundu ya anthu,+M’patseni Yehova ulemerero ndi kuvomereza kuti iye ndi wamphamvu.+   M’patseni Yehova ulemerero woyenera dzina lake.+Tengani mphatso ndi kulowa m’mabwalo ake.+   Gwadirani Yehova mutavala zovala zokongola ndi zopatulika.+Njenjemerani ndi mantha aakulu* pamaso pake, inu anthu nonse okhala padziko lapansi.+ 10  Nenani pakati pa anthu a mitundu ina kuti: “Yehova wakhala mfumu.+Dziko lapansi nalonso lakhazikika moti silingagwedezeke.+Iye adzaweruzira mitundu ya anthu milandu yawo mwachilungamo.”+ 11  Kumwamba kukondwere, ndipo dziko lapansi lisangalale.+Nyanja ichite mkokomo ndi zonse zimene zili mmenemo.+ 12  Mtunda ukondwere ndi zonse zimene zili kumeneko.+Pa nthawi imodzimodziyo, mitengo ya m’nkhalango ifuule mokondwera pamaso pa Yehova.+ 13  Pakuti iye wabwera.+Iye wabwera kudzaweruza dziko lapansi.+Adzaweruza dziko mwachilungamo,+Ndipo adzaweruza mitundu ya anthu mokhulupirika.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “imvani kupweteka kwambiri.”