Salimo 141:1-10

Nyimbo ya Davide. 141  Inu Yehova, ine ndakuitanani.+Bwerani kwa ine mofulumira.+Tcherani khutu pamene ndikukuitanani.+   Pemphero langa likhale lokonzedwa ngati zofukiza+ pamaso panu,+Mapembedzero anga akhale ngati nsembe yambewu yamadzulo.+   Inu Yehova, ikani mlonda pakamwa panga.+Ikani wolondera patsogolo pa milomo yanga.+   Musachititse mtima wanga kukonda choipa chilichonse,+Kuti ndisamachite zinthu zoipa zonditchukitsa,+Pamodzi ndi amene amachita zinthu zopweteka anzawo,+Kuti ndisadye chakudya chawo chapamwamba.+   Wolungama akandimenya ndiye kuti wandisonyeza kukoma mtima kosatha,+Ndipo akandidzudzula ndiye kuti wandidzoza mafuta pamutu panga,+Mafuta amene mutu wanga sungawakane.+Pakuti ndidzapemphererabe anthu olungama ngakhale pamene masoka awagwera.+   Oweruza awo awagwetsera pansi m’mphepete mwa thanthwe,+Koma anthu awo amva zonena zanga ndipo aona kuti ndi zabwino.+   Mafupa athu amwazika pakamwa pa Manda,Mofanana ndi zidutswa zimene zimamwazika pansi pamene munthu akuwaza ndi kung’amba mtengo.+   Koma ine maso anga ali pa inu+ Yehova Ambuye Wamkulu Koposa.+Ndathawira kwa inu.+Musalole kuti moyo wanga uwonongeke.+   Nditetezeni kuti ndisagwidwe pamsampha umene anditchera,+Kuti ndisakodwe ndi makhwekhwe a anthu ochita zopweteka anzawo.+ 10  Oipa onse adzagwera m’maukonde awo omwe,+Koma ine ndidzadutsa bwinobwino.

Mawu a M'munsi